Salimo
Nyimbo ya Asafu.+
50 Yehova, Mulungu wa milungu+ walankhula.
Iye akuitana anthu onse okhala padziko lapansi,
Kuchokera kotulukira dzuwa mpaka kumene limalowera.*
2 Mulungu wawala ali ku Ziyoni, mzinda wokongola kwambiri.+
3 Mulungu wathu adzabwera ndipo sangakhale chete.+
5 “Sonkhanitsani okhulupirika anga kwa ine,
Amene akuchita pangano ndi ine pogwiritsa ntchito nsembe.”+
6 Kumwamba kukulengeza kuti iye ndi wachilungamo,
Chifukwa Mulungu ndi Woweruza.+ (Selah)
7 “Ndimvereni anthu anga, ndipo ine ndilankhula,
Inu Aisiraeli, ine ndipereka umboni wotsutsana nanu.+
Ine ndine Mulungu, Mulungu wanu.+
8 Sindikukudzudzulani chifukwa cha nsembe zanu,
Kapena chifukwa cha nsembe zanu zopsereza zathunthu zimene mumapereka kwa ine nthawi zonse.+
10 Chifukwa nyama iliyonse yakutchire ndi yanga,+
Ngakhale nyama zopezeka mʼmapiri 1,000.
11 Ndikudziwa mbalame iliyonse ya mʼmapiri,+
Nyama zosawerengeka zakutchire ndi zanga.
12 Ngakhale nditakhala ndi njala, sindingakuuzeni,
Chifukwa dziko lonse ndiponso zonse zimene zili mmenemo ndi zanga.+
13 Kodi ndiyenera kudya nyama ya ngʼombe zamphongo
Kapena kumwa magazi a mbuzi?+
14 Yamikani Mulungu kuti ikhale ngati nsembe imene mukupereka kwa iye,+
Ndipo perekani kwa Wamʼmwambamwamba zimene mwalonjeza.+
15 Pa nthawi yamavuto mundiitane.+
Ine ndidzakupulumutsani, ndipo inu mudzandilemekeza.”+
16 Koma Mulungu adzauza woipa kuti:
19 Umagwiritsa ntchito pakamwa pako kufalitsa zinthu zoipa,
Ndipo lilime lako limalankhula zachinyengo.+
20 Umakhala pansi nʼkumanenera mʼbale wako zinthu zoipa,+
Umaulula zolakwa za* mwana wamwamuna wa mayi ako.
21 Utachita zinthu zimenezi, ine sindinalankhule kanthu,
Choncho unkaganiza kuti ndikuona zinthu ngati mmene iweyo ukuzionera.
Koma tsopano ndikudzudzula
Ndipo ndikuuza mlandu umene ndakupeza nawo.+
22 Ganizirani zinthu zimenezi, anthu oiwala Mulungu inu,+
Kuti ndisakukhadzulekhadzuleni popanda aliyense wokupulumutsani.