-
Yesaya 13:20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 MʼBabulo simudzakhalanso anthu,
Ndipo sadzakhalanso malo oti anthu nʼkukhalamo ku mibadwo yonse.+
Kumeneko Mluya sadzakhomako tenti yake
Ndipo abusa sadzagonekako ziweto zawo.
-
-
Yeremiya 50:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Chifukwa mtundu wina wa anthu wabwera kudzamuukira kuchokera kumpoto.+
Mtundu umenewu wasandutsa dziko lake kukhala chinthu chochititsa mantha.
Palibe aliyense amene akukhala mʼdzikoli.
Anthu ndiponso ziweto zathawa.
Zathawira kutali.”
-
-
Yeremiya 51:29Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
29 Dziko lidzagwedezeka ndi kunjenjemera,
Chifukwa Yehova adzachitira Babulo zimene akuganiza
Kuti dziko la Babulo likhale chinthu chochititsa mantha, lopanda munthu wokhalamo.+
-