-
Deuteronomo 8:12-14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Mukadzadya nʼkukhuta, kumanga nyumba zabwino nʼkukhalamo,+ 13 ngʼombe zanu ndi nkhosa zanu nʼkuchuluka, siliva ndi golide wanu nʼkuwonjezeka ndiponso nʼkukhala ndi zinthu zochuluka, 14 musakalole kuti mtima wanu ukayambe kunyada+ nʼkukuchititsani kuiwala Yehova Mulungu wanu amene anakutulutsani mʼdziko la Iguputo, mʼnyumba yaukapolo,+
-
-
Deuteronomo 8:17, 18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Ngati mumtima mwanu munganene kuti, ‘Chuma ichi ndachipeza chifukwa cha ntchito ya manja anga komanso mphamvu zanga,’+ 18 muzikumbukira kuti ndi Yehova Mulungu wanu amene amakupatsani mphamvu kuti mupeze chuma,+ pofuna kusunga pangano lake limene analumbira kwa makolo anu, ngati mmene zilili lero.+
-