Salimo
97 Yehova wakhala Mfumu!+
Dziko lapansi lisangalale.+
Zilumba zambiri zikondwere.+
2 Mitambo ndi mdima wandiweyani zamuzungulira.+
Maziko a mpando wake wachifumu ndi chilungamo komanso chiweruzo cholungama.+
4 Kungʼanima kwa mphezi zake kumaunika dziko.
Dziko lapansi limaona zimenezi ndipo limanjenjemera.+
5 Mapiri amasungunuka ngati phula pamaso pa Yehova,+
Pamaso pa Ambuye wa dziko lonse lapansi.
6 Kumwamba kumalengeza za chilungamo chake,
Ndipo mitundu yonse ya anthu imaona ulemerero wake.+
7 Onse amene akutumikira chifaniziro chilichonse achite manyazi,+
Amene amadzitama chifukwa cha milungu yawo yopanda pake.+
Muweramireni,* inu milungu yonse.+
8 Ziyoni wamva ndipo akusangalala,+
Matauni* a ku Yuda akukondwera
Chifukwa cha zigamulo zanu, inu Yehova.+
9 Chifukwa inu Yehova, ndinu Wamʼmwambamwamba woyenera kulamulira dziko lonse lapansi.
Ndinu wokwezeka kwambiri kuposa milungu ina yonse.+
10 Inu amene mumakonda Yehova, muzidana ndi zoipa.+
11 Kuwala kwaunikira olungama+
Ndipo owongoka mtima akusangalala.
12 Sangalalani chifukwa cha Yehova, olungama inu,
Ndipo yamikirani dzina lake loyera.*