November
Lamlungu, November 1
Iye wakudya chakudya ichi adzakhala ndi moyo kosatha.—Yoh. 6:58.
Popeza timatumikira Yehova, tili ndi chiyembekezo chodzapeza zinthu zonse zimene Adamu ndi Hava anataya monga moyo wosatha. Adamu ndi Hava analephera kutumikira Yehova chifukwa choti sankamukonda kwambiri. Koma Yehova anawalolabe kupitiriza kukhala ndi moyo, kubereka ana komanso kusankha okha njira yolerera ana awowo. Pasanapite nthawi yaitali, zinaonekeratu kuti zimene anasankha zinali zopusa kwambiri. Mwana wawo woyamba anapha m’bale wake ndipo anthu ambiri anali achiwawa komanso odzikonda. (Gen. 4:8; 6:11-13) Koma Yehova anakonza njira yopulumutsira ana a Adamu ndi Hava amene ankafunitsitsa kumutumikira. (Yoh. 6:38-40, 57) Apatu tingati Yehova anasonyeza chikondi komanso kuleza mtima. Mukamaphunzira zokhudza makhalidwe amenewa mudzayamba kukonda kwambiri Yehova. Mtima womukondawu udzakuthandizani kuti mudzipereke kwa Yehova n’kumapewa kuchita zimene Adamu ndi Hava anachita. w19.03 2 ¶3; 4 ¶9
Lolemba, November 2
Nonsenu mukhale . . . omverana chisoni.—1 Pet. 3:8.
Kuti tikhale omverana chisoni, tiyenera kuyesetsa kuti tizimvetsa mavuto amene anthu a m’banja lathu komanso mumpingo akukumana nawo. Tizichita zinthu moganizira achinyamata, anthu odwala, okalamba komanso amene aferedwa. Ndi bwino kuwafunsa mmene zinthu zilili pa moyo wawo. Akamafotokoza mavuto awo tiziwamvetsera bwino. Tiziwasonyeza kuti tikumvetsa mavuto amene akukumana nawo. Kenako tiziwathandiza m’njira yoyenera. Tikamatero tidzasonyeza kuti tili ndi chikondi chenicheni. (1 Yoh. 3:18) Koma tiyenera kuchita zinthu mozindikira pothandiza ena. Tikutero chifukwa chakuti zimene wina angachite akakumana ndi mavuto zimakhala zosiyana ndi zimene wina angachite. Ena amamasuka kufotokoza mavuto awo pomwe ena samasuka. Ndiye pothandiza anthu tiyenera kupewa kufunsa mafunso amene ena angachite nawo manyazi. (1 Ates. 4:11) Munthu amene akufotokoza mavuto ake akhozanso kunena zinthu zimene ifeyo sitingagwirizane nazo. Zikatero tiyenera kungovomereza kuti ndi mmene iwowo akumvera. Tiyenera kukhala ofulumira kumva koma odekha polankhula.—Mat. 7:1; Yak. 1:19. w19.03 19 ¶18-19
Lachiwiri, November 3
Ndinachita mantha kwambiri.—Neh. 2:2.
Kodi mumachita mantha kuuza anthu ena choonadi? Zitsanzo za anthu ena otchulidwa m’Baibulo zingatithandize pankhaniyi. Mwachitsanzo, Nehemiya ankagwira ntchito m’nyumba ya mfumu yamphamvu. Pa nthawi ina, iye anakhumudwa kwambiri atamva kuti mpanda komanso mageti a ku Yerusalemu zidakali zowonongeka. (Neh. 1:1-4) Nehemiya ayenera kuti anachita mantha pamene mfumu inamufunsa zimene zamukhumudwitsa. Iye anapemphera mwamsanga kenako n’kuyankha. Mfumu itamva zimene zinachitika inathandiza anthu a Mulungu. (Neh. 2:1-8) Chitsanzo china ndi cha Yona. Yehova atamutuma kuti akalalikire ku Nineve anachita mantha kwambiri moti anathawira kutali. (Yona 1:1-3) Koma Yehova anamuthandiza kuti agwire bwinobwino ntchitoyi. Uthenga umene Yona anapereka unathandiza kwambiri anthu a ku Nineve. (Yona 3:5-10) Nkhani ya Nehemiya ikusonyeza kuti kupemphera tisanayankhe kumathandiza kwambiri. Ndipo nkhani ya Yona ikusonyeza kuti Yehova akhoza kutithandiza kuti tizichita zimene akufuna ngakhale pamene tili ndi mantha. w19.01 11 ¶12
Lachitatu, November 4
Palibe amene anasiya nyumba, [kapena banja] chifukwa cha ine, ndi chifukwa cha uthenga wabwino, amene panopa sadzapeza zochuluka kuwirikiza maulendo 100 m’nthawi ino . . . ndipo m’nthawi imene ikubwerayo, adzapeza moyo wosatha.—Maliko 10:29, 30.
Tikayamba kutsatira mfundo za m’Baibulo, kachezedwe kathu ndi achibale komanso anthu ena kamasintha. Zili choncho chifukwa cha mfundo ina imene Yesu ananena m’pemphero yakuti: “Ayeretseni ndi choonadi. Mawu anu ndiwo choonadi.” (Yoh. 17:17) Mawu oti “ayeretseni” angatanthauzenso kuti “apatuleni kuti akhale apadera.” Tikayamba kuphunzira choonadi, timakhala osiyana ndi dzikoli chifukwa sititsatira zimene anthu ake amachita. Timasinthanso mfundo zimene timayendera choncho anthu sationa mmene ankationera. Moyo wathu umayendera mfundo zachoonadi cha m’Baibulo. Ngakhale kuti sitifuna kuyambitsa mikangano, anzathu komanso achibale athu ena angayambe kutisala kapena kutitsutsa. Koma ife sitidabwa nazo zimenezi chifukwa Yesu ananeneratu kuti: “Adani a munthu adzakhala a m’banja lake lenileni.” (Mat. 10:36) Anatitsimikiziranso kuti tikagula choonadi madalitso ake amakhala ambiri kuposa chilichonse chimene tingasiye. w18.11 6 ¶11
Lachinayi, November 5
Mipingo yonse ya anthu a mitundu ina [ikuyamikira].—Aroma 16:4.
Mtumwi Paulo ankayamikira abale ndi alongo ake ndipo ananena mawu osonyeza kuyamikirako. Nthawi zonse ankayamikira Mulungu m’mapemphero ake chifukwa cha abale ndi alongowo. Iye ankasonyezanso kuti amawayamikira m’makalata ake. Mwachitsanzo, m’mavesi 15 oyambirira a Aroma chaputala 16, Paulo anatchula Akhristu anzake okwana 27. Iye ananena kuti Purisika ndi Akula ‘anaika miyoyo yawo pachiswe chifukwa cha moyo wake’ komanso Febe ‘anateteza iyeyo ndiponso abale ambirimbiri.’ Paulo anayamikira abale ndi alongo akhama amenewa. (Aroma 16:1-15) Iye ankadziwa kuti abale ndi alongowa si angwiro. Koma m’mawu omaliza a kalata yake yopita kwa Aroma anangotchula makhalidwe awo abwino. Abale ndi alongowo ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri atamva zimene Paulo analembazo zikuwerengedwa mokweza mumpingo. Mosakayikira, izi zinathandiza kuti azigwirizana kwambiri ndi Paulo. Kodi inuyo mumalankhula kapena kuchita zinthu zosonyeza kuti mumayamikira zimene anthu mumpingo wanu amachita? w19.02 16 ¶8-9
Lachisanu, November 6
Sindidzasiya kukhala ndi mtima wosagawanika.—Yobu 27:5.
Popeza kuti si ife angwiro, kodi tiziganiza kuti sitingakhale ndi mtima wosagawanika? Mwina tingaganize choncho chifukwa choona kuti tili ndi mavuto ambiri ndipo timalakwitsa zinthu zina. Koma Yehova saganizira kwambiri zinthu zimene timalakwitsa. Paja Mawu ake amanena kuti: “Mukanakhala kuti mumayang’anitsitsa zolakwa, ndani akanaima pamaso panu, inu Yehova?” (Sal. 130:3) Iye amadziwa kuti si ife angwiro ndipo amatikhululukira ndi mtima wonse. (Sal. 86:5) Yehova amadziwanso zimene sitingakwanitse kuchita ndipo amayembekezera kuti tizingochita zimene tingakwanitse. (Sal. 103:12-14) Kukonda Mulungu n’kumene kungatithandize kuti tikhale ndi mtima wosagawanika. Tiyenera kukonda Mulungu ndiponso kukhala odzipereka kwa iye ndi mtima wonse. Tikamatero ngakhale titakumana ndi mayesero, tidzakhala ndi mtima wosagawanika komanso tidzakhala okhulupirika kwa Yehova. (1 Mbiri 28:9; Mat. 22:37) Timadziwa mfundo za Yehova ndipo timafuna kuchita zimene zimamusangalatsa. Chifukwa chomukonda timaika zofuna zake pamalo oyamba posankha zochita ndipo timasonyeza kuti tili ndi mtima wosagawanika. w19.02 3 ¶4-5
Loweruka, November 7
Uteteze mtima wako.—Miy. 4:23.
Nthawi iliyonse imene taona ubwino wochita zinthu zoyenera, chikhulupiriro chathu chimalimba. (Yak. 1:2, 3) Timamva bwino podziwa kuti Yehova akusangalala nafe ndipo mtima wofuna kumukondweretsa umakula. (Miy. 27:11) Mayesero alionse amene tingakumane nawo amatipatsa mwayi wosonyeza kuti timatumikira Yehova ndi mtima wonse. (Sal. 119:113) Timasonyeza kuti timakonda Yehova kuchokera pansi pa mtima ndipo timafunitsitsa kumvera malamulo ake komanso kuchita zimene amafuna. (1 Maf. 8:61) Popeza si ife angwiro, nthawi zina timalakwitsa zinthu. Zimenezi zikachitika, tizingokumbukira chitsanzo cha Mfumu Hezekiya. Nayenso analakwitsa zinthu zina. Koma iye analapa ndipo anapitiriza kutumikira Yehova “ndi mtima wathunthu.” (Yes. 38:3-6; 2 Mbiri 29:1, 2; 32:25, 26) Choncho tiyeni tiziyesetsa kupewa kusokonezeka ndi maganizo a Satana. Komanso tizipempha Yehova kuti atipatse “mtima womvera” ndiponso kuti tikhalebe okhulupirika.—1 Maf. 3:9; Sal. 139:23, 24. w19.01 18-19 ¶17-18
Lamlungu, November 8
Tiyeni nthawi zonse tizitamanda Mulungu. Tizichita zimenezi monga nsembe imene tikupereka kwa Mulungu, yomwe ndi chipatso cha milomo yathu. Timagwiritsa ntchito milomo imeneyi polengeza dzina lake kwa anthu ena.—Aheb. 13:15.
Kupereka ndemanga pamisonkhano kumatithandiza ifeyo. (Yes. 48:17) N’chifukwa chiyani tikutero? Choyamba, ngati tikufuna kukapereka ndemanga m’pamene timakonzekera bwino misonkhano. Ndipo tikamakonzekera bwino timayamba kumvetsa bwino Mawu a Mulungu. Ndiye tikamamvetsa bwino Baibulo m’pamene timatsatira kwambiri mfundo zimene taphunzira. Chachiwiri, timasangalala kwambiri ndi misonkhano chifukwa timayankha nawo. Chachitatu, popeza pamafunika kuchita khama kuti tiyankhe, mfundo zimene tinayankhazo sitiziiwala. Timasangalatsanso Yehova tikamafotokoza zimene timakhulupirira. Yehova amamvetsera tikamayankha pamisonkhano ndipo amayamikira zonse zimene timachita kuti tiyankhe. (Mal. 3:16) Tikamayesetsa kumusangalatsa amatidalitsa. (Mal. 3:10) Apa zikuonekeratu kuti tili ndi zifukwa zomveka zotichititsa kuyankha pamisonkhano. w19.01 8 ¶3; 9-10 ¶7-9
Lolemba, November 9
Nyansidwani ndi choipa, gwiritsitsani chabwino.—Aroma 12:9.
Yehova amachita zinthu motiganizira. M’malo motipatsa malamulo ambirimbiri, iye amatiphunzitsa moleza mtima kuti tizitsatira lamulo la chikondi. Iye amafuna kuti tiziyendera mfundo zake komanso kudana ndi zoipa. Chitsanzo chabwino cha mmene Yehova amatiphunzitsira ndi ulaliki wapaphiri wa Yesu. Tikutero chifukwa chakuti umafotokoza zimene zimachititsa kuti munthu achite zoipa. (Mat. 5:27, 28) Khristu, yemwe ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, adzapitiriza kutiphunzitsa tikadzalowa m’dziko latsopano kuti tizidzamutsanzira pa nkhani yokonda zabwino ndi kudana ndi zoipa. (Aheb. 1:9) Iye adzatithandizanso kuti matupi ndi maganizo athu akhale angwiro. Pa nthawiyo simudzavutikanso ndi uchimo kapena zotsatira zake. Kenako mudzasangalala ndi “ufulu waulemerero” umene Yehova wakulonjezani. (Aroma 8:21) Koma sikuti ufulu wathu m’dziko latsopano udzakhala wopanda malire. Tikutero chifukwa chakuti tizidzafunikabe kuchita zinthu mosonyeza kuti timakonda Mulungu ndi anzathu.—1 Yoh. 4:7, 8. w18.12 23 ¶19-20
Lachiwiri, November 10
Azimulembera kalata yothetsera ukwati ndi kum’patsa m’manja mwake, n’kumuchotsa panyumba pake.—Deut. 24:1.
Mwamuna wachiisiraeli ankaloledwa kuthetsa banja ngati ‘wam’peza mkazi wake ndi vuto linalake.’ Chilamulocho sichinafotokoze kuti “vuto” lake lingakhale lotani. Koma liyenera kuti linkakhala lalikulu kapena lochititsa manyazi kwambiri. (Deut. 23:14) N’zomvetsa chisoni kuti pofika nthawi ya Yesu, Ayuda ankathetsa mabanja “pa chifukwa chilichonse.” (Mat. 19:3) Ifeyo sitingafune m’pang’ono pomwe kutengera maganizo amenewa. Mneneri Malaki anafotokoza maganizo a Yehova pa nkhani yothetsa banja. Pa nthawiyo, amuna ankakonda kuthetsa mabanja ndi ‘akazi amene anawakwatira ali achinyamata’ mwina n’cholinga choti akwatire achitsikana, omwe n’kutheka kuti sankalambira Yehova. Ndiyeno pofotokoza maganizo a Yehova, Malaki analemba kuti: “Ndimadana ndi zakuti anthu azithetsa mabanja.” (Mal. 2:14-16) Zimenezi zikugwirizana ndi zimene Mawu a Mulungu amanena pa nkhani ya banja loyambirira. Paja amati: ‘Mwamuna adzadziphatika kwa mkazi wake, ndipo iwo adzakhala thupi limodzi.’ (Gen. 2:24) Yesu anatsindika maganizo a Atate akewa ponena kuti: “Chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.”—Mat. 19:6. w18.12 11 ¶7-8
Lachitatu, November 11
Zokolola n’zochuluka, koma antchito ndi ochepa.—Mat. 9:37.
Abale ndi alongo amatha kudzipereka kuti akatumikire kudera lakutali ndi kwawo. Iwo ali ndi mtima wofanana ndi wa mneneri Yesaya. Yehova atamufunsa kuti: “Kodi nditumiza ndani, ndipo ndani apite m’malo mwa ife?” iye anayankha kuti: “Ine ndilipo! Nditumizeni.” (Yes. 6:8) Kodi inunso mungakwanitse kudzipereka kukagwira ntchito kumene kukufunika thandizo? Ponena za ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa, Yesu ananena kuti: “Pemphani Mwini zokolola kuti atumize antchito kukakolola.” (Mat. 9:38) Kodi mungakachite upainiya kudera limene kukufunika ofalitsa ambiri? Kapena mwina mungathandize munthu wina kuti akachite zimenezi? Abale ndi alongo ambiri aona kuti njira yabwino yosonyezera kuti amakonda Mulungu ndi anzawo ndi kukachita upainiya kudera limene kukufunika olalikira ambiri. Nanga pali njira zinanso zimene mungawonjezere utumiki wanu? Mukachita zimenezi mudzakhala osangalala kwambiri. w18.08 27 ¶14-15
Lachinayi, November 12
Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama, koma mukhale okhutira ndi zimene muli nazo pa nthawiyo.—Aheb. 13:5.
Mabuku a Uthenga Wabwino amatithandiza kudziwa maganizo a Yehova pa nkhani ya chuma. Yehova anasankha banja losauka kuti lilere Mwana wake. (Lev. 12:8; Luka 2:24) Yesu atabadwa, Mariya anamugoneka “modyeramo ziweto, chifukwa anasowa malo m’nyumba ya alendo.” (Luka 2:7) Yehova akanafuna akanatha kupeza malo abwino oti Mwana wake abadwiremo. Koma anaona kuti chofunika kwambiri ndi banja lokonda zinthu zauzimu limene lingasamalire bwino Mwanayo. Nkhani ya kubadwa kwa Yesu ikutithandiza kudziwa maganizo a Yehova pa nkhani ya chuma. Makolo ambiri amayesetsa kuti ana awo adzakhale ndi chuma ndipo nthawi zina saganizira n’komwe za moyo wawo wauzimu. Koma Yehova amaona kuti zinthu zauzimu ndi zofunika kuposa chilichonse. Kodi inuyo mumayendera maganizo a Yehova pa nkhaniyi? Nanga zochita zanu zimasonyeza chiyani? w18.11 24 ¶7-8
Lachisanu, November 13
Odala ndi anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.—Sal. 144:15.
Yehova ndi wachimwemwe ndipo amafuna kuti nafenso tizisangalala. Amatipatsa zinthu zambiri zotithandiza kuti tikhale osangalala. (Deut. 12:7; Mlal. 3:12, 13) Koma zingakhale zovuta kuti munthu akhale wosangalala. Mavuto monga kuferedwa, kutha kwa banja, kusowa ntchito komanso kuchotsedwa kwa mnzathu angapangitse kuti tisamasangalale. Mavuto a m’banja komanso kusemphana maganizo zimachititsanso kuti tizikhala ndi nkhawa. Ena amasowa mtendere chifukwa chotsutsidwa ndi anzawo kuntchito kapena kusukulu ndipo ena amazunzidwa kapena kumangidwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Anthu angalepherenso kusangalala chifukwa cha matenda. Koma tizikumbukira kuti, Yesu Khristu yemwe amatchedwa “wachimwemwe ndi Wamphamvu yekhayo” ankakonda kuthandiza anthu kuti azisangalala. (1 Tim. 6:15; Mat. 11:28-30) Pa ulaliki wake wapaphiri, Yesu anatchula zinthu zingapo zimene zingatithandize kukhala osangalala ngakhale kuti timakumana ndi mavuto. w18.09 17-18 ¶1-3
Loweruka, November 14
Inu ndinu ana a Yehova Mulungu wanu. Musamadzichekecheke kapena kumeta nsidze zanu chifukwa cha anthu akufa.—Deut. 14:1.
Zimakhala zovuta kwambiri kuti munthu amene akuphunzira choonadi asiye miyambo ndi zikhalidwe zimene anazolowera. (Miy. 23:23) Ena amamvetsa zifukwa za m’Malemba zosiyira zinthuzi koma zimawavutabe chifukwa choopa achibale kapena anzawo. Nkhaniyi imavuta kwambiri ngati miyambo yake ndi yokhudza kulemekeza achibale amene anamwalira. Koma chitsanzo cha anthu ena pa nkhani yolimba mtima chingatithandize. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene Akhristu ena anachita ku Efeso mu nthawi ya atumwi. Kodi Akhristu amene anali atangophunzira kumene choonadi ku Efeso anatani kuti asiye zamatsenga? Baibulo limanena kuti: “Anasonkhanitsa mabuku awo pamodzi ndi kuwatentha pamaso pa onse. Ndipo atawonkhetsa mitengo yake, anapeza ndalama zasiliva zokwana 50,000. Choncho mawu a Yehova anapitiriza kufalikira ndi kugonjetsa zopinga zambiri.” (Mac. 19:19, 20) Akhristu okhulupirikawa atachita zimenezi anadalitsidwa kwambiri. w18.11 7 ¶15-16
Lamlungu, November 15
Atamaliza kuchita mdulidwe pamtundu wonsewo, anthuwo anakhala m’malo awo mumsasa mpaka atachira.—Yos. 5:8.
Aisiraeli atangowoloka mtsinje wa Yorodano, Yoswa anakumana ndi munthu atanyamula lupanga. Munthuyo anali ‘kalonga wa gulu lankhondo la Yehova,’ yemwe anali wokonzeka kuteteza anthu a Mulungu. (Yos. 5:13-15) Mngeloyo anapatsa Yoswa malangizo omveka bwino a mmene angagonjetsere mzinda wa Yeriko. Poyamba, malangizo ena akanaoneka ngati osathandiza. Mwachitsanzo, Yehova analamula kuti amuna onse adulidwe ndipo izi zikanachititsa kuti amunawo asathe kuchita chilichonse kwa masiku angapo. Ndiye funso n’kumati, ‘Kodi imeneyi inalidi nthawi yabwino yoti asilikali adulidwe?’ (Gen. 34:24, 25; Yos. 5:2) N’kutheka kuti asilikaliwo ankadzifunsa kuti, kodi adani atabwera panopa tingateteze bwanji mabanja athu? Koma kenako anangomva kuti “mzinda wa Yeriko unatsekedwa mwamphamvu chifukwa cha ana a Isiraeli.” (Yos. 6:1) Atangomva zimenezi ayenera kuti anazindikira kuti palibe chifukwa chokayikirira malangizo alionse amene Yehova angawapatse. w18.10 23 ¶5-7
Lolemba, November 16
Mukuchitiranji zimenezi? Ifenso ndife anthu okhala ndi zofooka ngati inu nomwe.—Mac. 14:15.
Kodi ifeyo tingatsanzire bwanji kudzichepetsa kwa Paulo? Choyamba, sitiyenera kufuna kapena kulola kuti anthu azitilemekeza mopitirira malire chifukwa cha zimene timachita mothandizidwa ndi Yehova. Aliyense angachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndimaona bwanji anthu amene ndimawalalikira? Kodi mwina ndayamba kutengera mtima watsankho n’kumanyoza anthu amtundu wina?’ Chosangalatsa n’chakuti a Mboni za Yehova padziko lonse akhala akuyesetsa kulalikira m’gawo lawo lonse kuti mwina angapeze anthu amene angamvetsere uthenga wabwino. Nthawi zina amaphunzira zilankhulo komanso zikhalidwe za anthu amene ena amawanyoza. Abale ndi alongo amene amachita zimenezi sayenera kudziona kuti ndi apamwamba kuposa anthuwo. Koma aziyesetsa kuwamvetsa n’cholinga choti aziwafika pamtima. w18.09 5 ¶9, 11
Lachiwiri, November 17
Yudasi Mgalileya . . . anakopa anthu ndipo anamutsatira.—Mac. 5:37.
Aroma analamula kuti Yudasi aphedwe. Panali Ayuda ambiri amene ankayembekezera kuti Mesiya akadzabwera adzawamasula ku ulamuliro wa Aroma komanso kuchititsa kuti mtundu wachiyuda ukhale wolemekezeka. (Luka 2:38; 3:15) Ambiri ankakhulupirira kuti Mesiya adzakhazikitsa ufumu ku Isiraeli ndipo zimenezi zikachitika, Ayuda okhala m’mayiko osiyanasiyana adzatha kubwerera kwawo. Kumbukirani kuti nthawi ina Yohane Mbatizi anafunsa Yesu kuti: “Kodi Mesiya amene tikumuyembekezera uja ndinu kapena tiyembekezere wina?” (Mat. 11:2, 3) N’kutheka kuti Yohane ankafuna kudziwa ngati panali wina amene adzachite zonse zimene Ayuda ankayembekezera. Nawonso ophunzira awiri a Yesu amene anakumana naye pamsewu wopita ku Emau ankayembekezera kuti Mesiya achita zinthu zinazake zothandiza Isiraeli. (Luka 24:21) Atumwi a Yesu anamufunsanso kuti: “Ambuye, kodi mubwezeretsa ufumu kwa Isiraeli pa nthawi ino?”—Mac. 1:6. w18.06 4 ¶3-4
Lachitatu, November 18
Munthu amene sadziwa zinthu amakhulupirira mawu alionse.—Miy. 14:15.
Tiyenera kusamala kwambiri tikapeza nkhani zokhudza anthu a Yehova. Tisaiwale kuti Satana amaneneza atumiki a Mulungu okhulupirika. (Chiv. 12:10) M’pake kuti Yesu anachenjeza kuti adani athu ‘adzatinamizira zoipa zilizonse.’ (Mat. 5:11) Tikamakumbukira chenjezoli sitingadabwe tikamva nkhani zabodza zokhudza anthu a Yehova. Kodi inuyo mumakonda kutumiza maimelo ndiponso mameseji kwa anzanu? Ngati zili choncho, mwina mukamva nkhani inayake yatsopano mungafune kukhala ngati mtolankhani amene amayesetsa kukhala woyamba kufalitsa nkhaniyo. Komabe musanatumize meseji kapena imeloyo, muyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndatsimikizira kuti nkhaniyi ndi yoona? Kodi ndikudziwadi mfundo zonse?’ Ngati simunatsimikizire, mukhoza kufalitsa nkhani zabodza kwa abale ndi alongo. Ndipo ngati mukukayikira, mungachite bwino osatumiza. w18.08 3 ¶3; 4 ¶6-7
Lachinayi, November 19
Khalani opatsa ndipo inunso anthu adzakupatsani.—Luka 6:38.
Yesu amafuna kuti tizikhala osangalala choncho anatilimbikitsa kuti tikhale opatsa. Anthu ambiri akapatsidwa zinthu nawonso amachita zabwino. N’zoona kuti anthu ena sayamikira. Koma akayamikira, zimathandiza kuti nawonso akhale opatsa. Choncho muziyesetsa kukhala opatsa ngakhale kuti anthu ena sayamikira. Zimene mungapatse ena zikhoza kuthandiza kwambiri ngakhale mutangowapatsa kamodzi kokha. Anthu amene amapereka zinthu kuchokera pansi pa mtima sakhala ndi cholinga choti adzapezepo kenakake. Yesu ankaganizira mfundoyi pamene ananena kuti: “Ukakonza phwando, uziitana anthu osauka, otsimphina, olumala, ndi akhungu. Ukatero udzakhala wodala, chifukwa alibe choti adzabweze.” (Luka 14:13, 14) Wolemba Baibulo wina ananena kuti munthu wopatsa “adzadalitsidwa.” Winanso ananena kuti: “Wodala ndi munthu amene amachita zinthu moganizira munthu wonyozeka.” (Miy. 22:9; Sal. 41:1) Choncho, tiyenera kukhala opatsa chifukwa timasangalala tikamathandiza anthu. w18.08 21-22 ¶15-16
Lachisanu, November 20
Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usadalire luso lako lomvetsa zinthu. Uzim’kumbukira m’njira zako zonse, ndipo iye adzawongola njira zako.—Miy. 3:5, 6.
Popeza nkhani zabodza zimapezeka paliponse masiku ano komanso anthufe si angwiro, timavutika kudziwa mfundo zonse pa nkhani inayake ndiponso kuzimvetsa bwino. Koma n’chiyani chingatithandize? Tiyenera kudziwa mfundo za m’Baibulo komanso kuzitsatira. Mfundo ina yofunika ndi yakuti munthu akayankhira nkhani asanaimvetsetse amapusa komanso amachita manyazi. (Miy. 18:13) Palinso mfundo ina ya m’Baibulo imene imatikumbutsa kuti tisamangokhulupirira mawu aliwonse. (Miy. 14:15) Mfundo inanso ndi yakuti kaya timadziwa zambiri bwanji, tiyenera kupewa kudalira luso lathu lomvetsa zinthu. Mfundo za m’Baibulo zingatiteteze ngati timayesetsa kupeza mfundo zoona pa nkhani inayake, kuziganizira bwino komanso kusankha zochita mwanzeru. w18.08 7 ¶19
Loweruka, November 21
Kodi sitiyenera kuwagonjera [Atate wa moyo wathu wauzimu]?—Aheb. 12:9.
Njira imodzi imene timasonyezera kuti timayamikira zimene Yehova watichitira ndi kudzipereka kwa iye ndi mtima wonse. Munthu akabatizidwa, amasonyeza poyera kuti iyeyo ndi wa Yehova ndipo ndi wokonzeka kumugonjera. Izi n’zimene Yesu anachita pamene anabatizidwa, chifukwa zinali ngati ankauza Yehova kuti: “Ndimakondwera ndi kuchita chifuniro chanu, inu Mulungu wanga.” (Sal. 40:7, 8) Kodi Yehova anatani pamene Yesu anabatizidwa? Baibulo limanena kuti: “Atabatizidwa, nthawi yomweyo Yesu anavuuka m’madzimo. Pamenepo kumwamba kunatseguka, ndipo Yohane anaona mzimu wa Mulungu ukutsika ngati nkhunda kudzamutera. Panamvekanso mawu ochokera kumwamba onena kuti: ‘Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwera naye.’” (Mat. 3:16, 17) Ngakhale kuti Yesu anali kale Mwana wake, Yehova anasangalala kumuona akudzipereka ndi mtima wonse kuti achite chifuniro chake. Yehova amasangalalanso akaona tikudzipereka kwa iye ndipo amatidalitsa.—Sal. 149:4. w18.07 23 ¶4-5
Lamlungu, November 22
Kodi tichite kukutulutsirani madzi m’thanthweli?—Num. 20:10.
Ponena kuti “tichite” kukutulutsirani, Mose ayenera kuti ankatanthauza iyeyo ndi Aroni. Ponena zimenezi, iye sanalemekeze Yehova monga wochititsa zozizwitsazo. Tikhoza kutsimikizira kuti mfundoyi ndi yoona tikaganizira zimene lemba la Salimo 106:32, 33 limanena. Paja limati: “Iwo anaputa mkwiyo pa madzi a ku Meriba, moti Mose sizinamuyendere bwino chifukwa cha anthu amenewa. Iwo anamukwiyitsa ndipo Mose anayamba kulankhula mosalingalira bwino.” (Num. 27:14) Kaya zinthu zinali bwanji, koma zimene Mose anachitazi zinachititsa kuti anthu asapereke ulemu woyenerera kwa Yehova. Choncho Yehova anauza Mose ndi Aroni kuti: “Amuna inu munapandukira malangizo anga.” (Num. 20:24) Apa zikuonekeratu kuti tchimo lawoli linali lalikulu kwambiri. Yehova anali atanena kale kuti m’badwo wonse wa Aisiraeli sudzalowa m’dziko la Kanani chifukwa chosamumvera. (Num. 14:26-30, 34) Choncho Yehova anachita zinthu moyenera komanso mwachilungamo popereka chiweruzo chomwecho kwa Mose pamene nayenso sanamumvere. Iye sanaloledwe kulowa m’Dziko Lolonjezedwa. w18.07 14 ¶9, 12; 15 ¶13
Lolemba, November 23
Ndi bwino kusadya nyama kapena kusamwa vinyo kapena kusachita kalikonse kamene kamakhumudwitsa m’bale wako.—Aroma 14:21.
Tiyerekeze kuti muli ndi ufulu wochita zinthu zinazake koma munthu wina akhoza kukhumudwa nazo, kodi mungalolere kuti musazichite? N’zosakayikitsa kuti mungapewe kuchita zinthuzo. Mwachitsanzo, abale athu ena asanakhale a Mboni ankamwa mowa mopitirira malire ndipo panopa safuna kumwa ngakhale pang’ono. Ndiye tonsefe sitingafune kuchititsa munthu kuti ayambirenso zinthu zimene zingamubweretsere mavuto. (1 Akor. 6:9, 10) Choncho ngati m’bale wabwera kwathu n’kukana mowa, si bwino kumukakamiza kuti amwe. Chitsanzo chabwino ndi zimene Timoteyo anachita poopa kukhumudwitsa Ayuda amene ankafuna kuwalalikira. Iye atatsala pang’ono kukwanitsa zaka 20 kapena atakwanitsa, analolera kuti adulidwe ngakhale kuti zinali zopweteka kwambiri. Maganizo ake anali ofanana ndi a mtumwi Paulo. (Mac. 16:3; 1 Akor. 9:19-23) Kodi nanunso mungalolere zinthu zinazake n’cholinga choti musakhumudwitse anthu ena? w18.06 18-19 ¶12-13
Lachiwiri, November 24
Ndidzapatsa mitundu ya anthu chilankhulo choyera.—Zef. 3:9.
Yehova amakoka anthu amtima wabwino mwapang’onopang’ono kuti ayambe kumulambira n’kukhala m’banja lake lauzimu. (Yoh. 6:44.) Mukakumana koyamba ndi munthu amene si wa Mboni, kodi mumadziwa zotani zokhudza munthuyo? Mumadziwa zochepa, mwina dzina ndi maonekedwe ake basi. Koma si mmene zimakhalira mukakumana ndi munthu amene amadziwa Yehova komanso kumukonda. Ngakhale kuti mumasiyana naye dziko, mtundu kapena chikhalidwe, mumadziwa zambiri zokhudza iyeyo ndipo iyenso amadziwa zambiri zokhudza inuyo. Mwachitsanzo, ngakhale kuti mumalankhula zilankhulo zosiyana, nonse mumadziwa “chilankhulo choyera.” Choncho aliyense amadziwa zimene mnzake amakhulupirira zokhudza zinthu monga Mulungu, makhalidwe abwino ndiponso zimene tikuyembekezera m’tsogolo. Ndipotu zimenezi ndi mfundo zofunika kwambiri kuzidziwa chifukwa ndi zimene zingakuthandizeni kukhulupirira munthu. Zimakuthandizaninso kuti muzigwirizana naye kwambiri. w18.12 21 ¶9-10
Lachitatu, November 25
Mukapanda kudulidwa . . . simungapulumuke.—Mac. 15:1.
Khristu anatsogolera bungwe lolamulira kuti lipereke malangizo akuti sizinali zofunika kuti Akhristu azidulidwa. (Mac. 15:19, 20) Koma kwa zaka zambiri pambuyo posankha zimenezi, Akhristu achiyuda ambiri ankapitiriza kuonetsetsa kuti ana awo akudulidwa. Koma tikhoza kudzifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani Yesu analola kuti nkhani ya mdulidweyi ipitirirebe kwa zaka zambiri ngakhale kuti imfa yake inathetsa Chilamulo cha Mose?’ (Akol. 2:13, 14) Anthu ena zimawatengera nthawi kuti azolowere kusintha kwa zinthu. Mwachitsanzo, Akhristu achiyuda ankafunika nthawi yaitali ndithu kuti ayambe kuona zinthu moyenera. (Yoh. 16:12) Ena zinawavuta kuti asiye kuona mdulidwe ngati chizindikiro choti anali pa ubwenzi wapadera ndi Mulungu. (Gen. 17:9-12) Pomwe ena amene ankakhala m’dera lomwe Ayuda ambiri ankakhala ankaopa kuti azizunzidwa ngati atamachita zinthu mosiyana ndi Ayudawo. (Agal. 6:12) Koma patapita nthawi, Khristu anapereka malangizo ena pogwiritsa ntchito Paulo kuti alembe makalata.—Aroma 2:28, 29; Agal. 3:23-25. w18.10 24-25 ¶10-12
Lachinayi, November 26
Kayafa . . . analangiza Ayuda . . . kuti kunali kopindulitsa kwa iwo kuti munthu mmodzi afere anthu onse.—Yoh. 18:14.
Kayafa anatumiza asilikali kuti akagwire Yesu usiku. Yesu ankadziwa za chiwembuchi choncho pa nthawi imene ankadya chakudya chamadzulo chomaliza ndi atumwi ake, anawauza kuti apeze malupanga. Malupanga awiri anali okwanira kuti awaphunzitse mfundo ina yofunika kwambiri. (Luka 22:36-38) Usiku wa tsiku limenelo, Petulo anagwiritsa ntchito lupanga limodzi n’kuvulaza munthu wina amene anali m’gulu limene linabwera kudzagwira Yesu. N’zosachita kufunsa kuti iye anapsa mtima poona kuti anthu akugwira Yesu usikuwo. (Yoh. 18:10) Koma Yesu anauza Petulo kuti: “Bwezera lupanga lako m’chimake, pakuti onse ogwira lupanga adzafa ndi lupanga.” (Mat. 26:52, 53) Zimene Yesu ananenazi zinali zogwirizana ndi mfundo imene iye anaipempherera usiku womwewo yakuti ophunzira akewo sayenera kukhala mbali ya dziko. (Yoh. 17:16) Mulungu ndi amene ali ndi udindo wolimbana ndi zinthu zopanda chilungamo. Ndipo ifeyo timapitiriza kukhala mwamtendere komanso mogwirizana. Popeza anthu ndi ogawikana m’dzikoli, Yehova ayenera kuti amasangalala kwambiri akamaona mgwirizano wa anthu ake.—Zef. 3:17. w18.06 7 ¶13-14, 16
Lachisanu, November 27
Chinjokacho chinakwiya ndi mkazi uja, moti chinapita kukachita nkhondo ndi otsala a mbewu yake.—Chiv. 12:17.
Kuwonjezera pa kunyengerera anthu, nthawi zina Satana amaopseza anthu kapena kuwazunza kuti asiye kukhala okhulupirika kwa Yehova. Mwachitsanzo, angachititse kuti maboma aletse ntchito yathu yolalikira. Apo ayi, akhoza kuchititsa anzathu akuntchito kapena kusukulu kuti azitinyoza chifukwa choti timatsatira mfundo za m’Baibulo. (1 Pet. 4:4) Akhozanso kuchititsa kuti achibale athu azitiletsa kupita kumisonkhano. (Mat. 10:36) Kodi n’chiyani chingatithandize ngati zimenezi zitatichitikira? Choyamba, sitiyenera kudabwa ndi zimenezi chifukwa Baibulo limasonyeza kuti Satana akulimbana nafe. (Chiv. 2:10) Chachiwiri, tiyenera kukumbukira nkhani yaikulu. Paja Satana amanena kuti anthufe timatumikira Yehova pokhapokha ngati zinthu zikutiyendera bwino. Iye amanena kuti tikhoza kusiya kumutumikira ngati tapanikizika ndi zinazake. (Yobu 1:9-11; 2:4, 5) Pomaliza, tiyenera kudalira Yehova kuti azitithandiza. Tizikumbukira lonjezo lake lakuti sadzatisiya ngakhale pang’ono.—Aheb. 13:5. w18.05 26 ¶14
Loweruka, November 28
Sukudziwa pamene padzachite bwino.—Mlal. 11:6.
Ngakhale pamene zikuoneka kuti uthenga wa Ufumu sukuwafika anthu pamtima, sitiyenera kuganiza kuti ntchito yathu yofesa mbewu ikupita pachabe. N’zoona kuti anthu ambiri samvetsera uthenga wathu koma amaona zimene timachita. Amaona kuti timavala bwino, ndife aulemu komanso timakonda kumwetulira. Anthu akaona khalidwe lathu labwino akhoza kuzindikira kuti zinthu zoipa zimene ankatiganizira si zoona. Zoterezi n’zimene zinachitikira Sergio ndi Olinda amene ndi apainiya. Iwo anati: “Pa nthawi ina sitinkamva bwino m’thupi ndipo sitinapite pamalo aja kwa nthawi ndithu. Titayambiranso kupita, anthu ena anatifunsa kuti, ‘Munasowatu. Chinachitika n’chiyani?’” Choncho ngati timachita khama, osalola kuti dzanja lathu lipume pa ntchito yofesa mbewu za Ufumu, timathandiza kwambiri pochitira “umboni ku mitundu yonse.” (Mat. 24:14) Koposa zonse, timasangalala podziwa kuti tikusangalatsa Yehova chifukwa iye amakonda anthu onse amene ‘amabereka zipatso mopirira.’—Luka 8:15. w18.05 16 ¶16-18
Lamlungu, November 29
Atamandike Mulungu . . . [amene] amatitonthoza m’masautso athu onse.—2 Akor. 1:3, 4.
Kungoyambira pamene anthu anachimwa, Yehova wakhala akusonyeza kuti ndi Mulungu wolimbikitsa. Adamu ndi Hava atangochimwa, Yehova anapereka lonjezo lolimbikitsa kwa ana a Adamu. Anasonyeza kuti zimene zinachitikazo sanali mapeto a zonse. Lonjezo la pa Genesis 3:15 limapatsa anthu chiyembekezo chakuti “njoka yakaleyo,” yemwe ndi Satana Mdyerekezi, adzawonongedwa pamodzi ndi ntchito zake zonse. (Chiv. 12:9; 1 Yoh. 3:8) Nowa ankakhala m’dziko la anthu osaopa Mulungu ndipo iye yekha ndi banja lake ndi amene ankalambira Yehova. Chiwawa ndi chiwerewere zinali ponseponse moti Nowa akanatha kukhumudwa kwambiri. (Gen. 6:4, 5, 9, 11; Yuda 6) Koma Yehova anamuuza kuti adzawononga anthu onse oipa ndipo anamuuzanso zoyenera kuchita kuti iye ndi banja lake apulumuke. (Gen. 6:13-18) Apatu Yehova anathandiza kwambiri Nowa ndipo anamulimbikitsa. w18.04 15 ¶1-2
Lolemba, November 30
Pitirizani kutonthozana ndi kulimbikitsana monga mmene mukuchitira.—1 Ates. 5:11.
Si nzeru kuganiza kuti ifeyo sitingalimbikitse munthu chifukwa choti timasowa chonena pocheza ndi anthu. Tikutero chifukwa chakuti kulimbikitsa munthu sikufuna zambiri. Ngakhale tikangomwetulira popereka moni kwa munthu timakhala titamulimbikitsa. Ngati munthu winayo wayankha moniyo popanda kumwetuliranso zingasonyeze kuti mwina pali vuto linalake. Ndiyeno kumumvetsera munthu woteroyo kungamulimbikitse kwambiri. (Yak. 1:19) Tonsefe tikhoza kulimbikitsa munthu amene akuda nkhawa. Paja Mfumu Solomo analemba kuti: “Mawu onenedwa pa nthawi yoyenera ndi abwino kwambiri. Maso owala amapangitsa mtima kusangalala. Uthenga wabwino umanenepetsa mafupa.” (Miy. 15:23, 30) Paulo anasonyeza kuti kuimba nyimbo za Ufumu limodzi kumalimbikitsanso. (Mac. 16:25; Akol. 3:16) Pamene tsiku la Yehova “likuyandikira,” anthufe tizifunika kulimbikitsana kwambiri.—Aheb. 10:25. w18.04 23 ¶16; 24 ¶18-19