Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 10/15 tsamba 9-13
  • Nchifukwa Ninji Tiyenera Kuwopa Mulungu Woona Tsopano?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nchifukwa Ninji Tiyenera Kuwopa Mulungu Woona Tsopano?
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chisonyezero cha Mphamvu Chozizwitsa
  • Kusonyeza Mantha Athu kwa Mulungu
  • Zotulukapo za Kuwopa Mulungu Tsopano
  • Opani Yehova Ndipo Lemekezani Dzina Lake Loyera
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Khalani ndi Mtima Woopa Yehova
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Kuwopa Mulungu Kodi Kungakupindulitseni?
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Nchifukwa Ninji Tiyenera Kuwopa Mulungu?
    Nsanja ya Olonda—1989
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 10/15 tsamba 9-13

Nchifukwa Ninji Tiyenera Kuwopa Mulungu Woona Tsopano?

“Opa[ni] Mulungu [woona, NW], musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.”​—MLALIKI 12:13.

1, 2. Kodi nchifukwa ninji mantha abwino kwa Mulungu ali oyenera?

KUWOPA Mulungu kwabwino ndi kwaulemu kuli bwino kwa munthu. Inde, ngakhale kuti mantha ambiri aumunthu amasokoneza malingaliro ngakhale kuvulaza thanzi lathu, kuli bwino kwa ife kuwopa Yehova Mulungu.​—Salmo 112:1; Mlaliki 8:12.

2 Mlengi amadziŵa zimenezi. Chifukwa cha chikondi chake pa zolengedwa zake, akulamula onse kumuwopa ndi kumulambira. Timaŵerenga kuti: “Ndinaona mngelo wina alikuuluka pakati pa mlengalenga, wakukhala nawo uthenga wabwino wosatha, aulalikire kwa iwo akukhala padziko, ndi kwa mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu; ndikunena ndi mawu aakulu, Opani Mulungu, mpatseni ulemerero; pakuti yafika nthaŵi ya chiweruziro chake; ndipo mlambireni Iye amene analenga m’mwamba ndi mtunda.”​—Chivumbulutso 14:6, 7.

3. Kodi Mlengi wathu anawachitira chiyani makolo athu oyamba?

3 Mosakayikira sitiyenera kunyalanyaza Mlengi wa zinthu zonse, Magwero a moyo, pakuti ndife ake pamodzi ndi pulanetili. (Salmo 24:1) Posonyeza chikondi chake chachikulu, Yehova anapatsa ana ake a padziko lapansi moyo ndi kuwapatsa malo abwino koposa okhalamo​—paradaiso wokongola. Komabe, mphatso yabwino kopambana imeneyi inali ndi zofuna zake. Kwenikweni, inaperekedwa kuti aisamalire. Makolo athu oyamba anafunikira kusamalira mudzi wawo wokhalamo ndi kuufutukula mpaka atadzaza dziko ndi kuligonjetsa. Anali ndi ufulu ndi mathayo pa nyama za pamtunda, mbalame, ndi nsomba​—zolengedwa zina zonse zimene zikanakhala m’dziko pamodzi nawo ndi mbadwa zawo. Pa choikizidwa chachikulu chimenechi, munthu anayenera kulangidwa ngati sanachisamalire.

4. Kodi munthu wachitanji ku chilengedwe cha Mulungu?

4 Mosasamala kanthu za chiyambi chabwino koposa chimenecho, taonani zimene munthu wachita kuipitsa mudzi wake wokongola wa dziko lapansi! Monyozera umwini wa Mulungu wa mphatso yokongola imeneyi, anthu adetsa dziko lapansi. Kuipitsako kwafika poti nkuwopseza moyo wa zinyama, mbalame, ndi nsomba za mitundu yambirimbiri. Mulungu wathu wachilungamo ndi wachikondi sadzalekerera kusakhulupirika kumeneku. Kuwononga dziko lapansi kukufuna kubwezera chilango, chinthu chimene ambiri akuwopa. Komabe, kuli kotonthoza kwa awo amene amadalira Mulungu kudziŵa zimene zidzachitika. Yehova adzabwezera chilango, ndipo dziko lapansi lidzabwezeretsedwa. Umenewu ulidi uthenga wabwino kwa olungama onse pa dziko lapansi.

5, 6. Kodi Yehova adzachitapo chiyani pa zimene munthu wachitira chilengedwe Chake?

5 Kodi ndi m’njira yotani imene Mulungu adzachiperekera chiweruzo chake? Kupyolera mwa Yesu Kristu, amene tsopano wakhazikitsidwa monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu wakumwamba. Kupyolera mwa Mwana wakumwamba ameneyo, Yehova adzathetsa dongosolo lodetsedwa, lopanduka lilipoli. (2 Atesalonika 1:6-9; Chivumbulutso 19:11) M’njira imeneyi iye adzetsera mpumulo kwa awo amene amamuwopa ndipo, panthaŵi imodzimodziyo, kupulumutsa ndi kusunga mudzi wathu wa dziko lapansi.

6 Kodi zimenezi zidzachitika motani? Baibulo limasimba za chisautso chachikulu chilinkudzacho chimene chidzafika pachimake m’nkhondo ya Armagedo. (Chivumbulutso 7:14; 16:16) Chimenechi chidzakhala chiweruzo cha Mulungu pa dongosolo loipitsidwali ndi oliipitsa ake. Kodi padzatsala anthu ena amoyo? Inde! Adzakhala awo amene amasonyeza kuwopa Mulungu, osati koipa, kodwazika, koma kwaulemu ndi koyenera. Iwo adzapulumuka.​—Miyambo 2:21, 22.

Chisonyezero cha Mphamvu Chozizwitsa

7. Kodi nchifukwa ninji Mulungu analoŵererapo m’malo mwa Israyeli m’tsiku la Mose?

7 Ntchito yachilendo imeneyi ya Yehova Mulungu inachitiridwa chithunzi ndi chinthu champhamvu chimene anachitira alambiri ake zaka 1,500 Nyengo Ino isanafike. Ulamuliro wa Igupto wamphamvu kwambiri pa zankhondo unamanga ukapolo antchito ake Achiisrayeli ochokera kunja, ngakhale kuyesa kufafaniza mtundu wonse mwambanda pamene wolamulira wake, Farao, analamula kuphedwa kwa makanda onse achimuna obadwa chatsopano Achiisrayeli. Chipambano cha Mulungu pa Igupto chinamasula Israyeli ku dongosolo lodidikiza la ndalelo, inde, kumasulidwa ku mtundu woipitsidwa ndi kulambira milungu yambiri.

8, 9. Kodi ndimotani mmene Mose ndi Aisrayeli anachitira pa kuloŵererapo kwa Mulungu?

8 Eksodo chaputala cha 15 akusimba za mmene Aisrayeli anachitira ndi chimasuko chawo ku Igupto. Kupenda chochitika chimenechi kudzatithandiza kumvetsetsa mmene Akristu angaomboledwere ku dongosolo lodetsedwa mwauzimu ndi mwakuthupi lilipoli. Tiyeni tipende Eksodo 15, tikumasumika maganizo pa mavesi osankhidwa kuti tiphunzire chifukwa chimene tiyenera kusankhira kuwopa Yehova, Mulungu woona. Tiyeni tiyambe ndi mavesi 1 ndi 2:

9 “Pamenepo Mose ndi ana a Israyeli anaimbira Yehova nyimbo iyi, nanena, ndi kuti, Ndizaimbira Yehova pakuti wapambanatu; kavalo ndi wokwera wake anawaponya m’nyanja. Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, ndipo wakhala chipulumutso changa.”

10. Kodi chinachititsa Mulungu kuwononga magulu ankhondo a Aaigupto nchiyani?

10 Anthu pa dziko lonse lapansi amadziŵa nkhaniyi ya mmene Yehova anamasulira Israyeli ku Igupto. Anadzetsa miliri pa ulamuliro wamphamvu wa dziko lonse mpaka Farao analola Aisrayeli kupita. Komabe magulu ankhondo a Farao anathamangira anthu opanda chitetezo amenewo ndipo anachita ngati kuti awatsekereza pa Nyanja Yofiira. Ngakhale zinachita ngati kuti ana a Israyeli adzataya ufulu wawo wopezedwa chatsopano, Yehova anali ndi chinachake m’malingaliro. Anatsegula njira pakati pa nyanja modabwitsa ndi kupulumutsa anthu ake. Pamene Aaigupto anatsatira, iye anatseka Nyanja Yofiira ndi kumiza Farao ndi magulu ake ankhondo.​—Eksodo 14:1-31.

11. Kodi nchiyani chimene chinatulukapo pa zimene Mulungu anachita pa Igupto?

11 Kuwononga kwa Yehova magulu ankhondo Achiigupto kunamkweza pamaso pa alambiri ake ndipo kunachititsa dzina lake kudziŵika konsekonse. (Yoswa 2:9, 10; 4:23, 24) Inde, dzina lake linakwezedwa pamwamba pa milungu yopanda mphamvu, yonyenga ya Igupto, imene inalephera kupulumutsa alambiri ake. Chidaliro chawo mwa milungu yawo ndi mwa munthu wokhoza kufa ndiponso mwa mphamvu ya zankhondo chinawagwiritsa mwala kwambiri. (Salmo 146:3) Nchifukwa chake Aisrayeli anasonkhezereka kuyimba zitamando zimene zinasonyeza mantha abwino kwa Mulungu wamoyo, amene amawombola anthu ake mwamphamvu!

12, 13. Kodi tiyenera kuphunziraponji pa chipambano cha Mulungu pa Nyanja Yofiira?

12 M’njira imodzimodziyo, tiyenera kudziŵa kuti palibe milungu yonama ya m’nthaŵi yathu ndipo palibe ulamuliro wamphamvu koposa, ngakhale wokhala ndi zida za nyukiliya, umene ungalingane ndi Yehova. Iye akhoza ndipo adzawombola anthu ake. “Achita mwa chifuniro chake m’khamu la kumwamba ndi mwa okhala pa dziko lapansi; ndipo palibe woletsa dzanja lake, kapena wakunena naye, Muchitanji?” (Danieli 4:35) Pamene timvetsetsa mawuŵa, nafenso timasonkhezereka kuimba zitamando zake mokondwa.

13 Nyimbo ya chipambano pa Nyanja Yofiira ikupitiriza kuti: “Yehova ndiye wankhondo; dzina lake ndiye Yehova.” Motero, Wankhondo wosagonjetseka ameneyu, saali chinthu chosadziŵika dzina lake chongopekedwa ndi munthu. Ali ndi dzina! Iye ndiye ‘Amene amachititsa kukhalako,’ Mpangi Wamkulu, Iye Amene ‘dzina lake ndilo Yehova, . . . Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.’ (Eksodo 3:14; 15:3-5; Salmo 83:18) Kodi simuvomereza kuti kukanakhala kwanzeru kwa Aaigupto akalewo kukhala ndi mantha kwa Wamphamvuyonse m’malo mwa kumunyoza?

14. Kodi kufunika kwa mantha aumulungu kunasonyezedwa motani pa Nyanja Yofiira?

14 Monga Mlinganizi wa dziko lapansi, Mpangi wa nyanja ali ndi ulamuliro wonse pa madzi. (Eksodo 15:8) Mwa kugwiritsiranso ntchito ulamuliro wake pa mphepo, anachita zimene zinaoneka kukhala zosatheka. Anapatula madzi ambiriwo pamalo ena ake ndi kuwakankhira kumbuyo kotero kuti apange njira pakati pa madzi yoti anthu ake apitemo. Pangani chithunzi cha chochitikacho m’maganizo mwanu: mamiliyoni a matani a madzi a m’nyanja ounjikana kupanga makhoma oima chiriri, akumapanga njira yotetezereka yothaŵiramo Israyeli. Inde, awo amene anasonyeza mantha abwino kwa Mulungu anatetezeredwa. Ndiyeno Yehova analola madzi kubwerera ngati liyambwe lalikulu, akumamiza magulu ankhondo a Farao ndi zida zawo zonse. Ha, nchisonyezero champhamvu yaumulungu chotani nanga pa milungu yopanda pake ndi mphamvu ya zankhondo ya anthu! Mosakayikira, Yehova ndiye ayenera kuwopedwa, sichoncho kodi?​—Eksodo 14:21, 22, 28; 15:8.

Kusonyeza Mantha Athu kwa Mulungu

15. Kodi tiyenera kuchitapo chiyani pa zochita ndi zamphamvu zopulumutsa za Mulungu?

15 Tikanaima ndi Mose tili osungika, mosakayikira tikanasonkhezereka kuimba kuti: “Afanana ndi inu ndani mwa milungu, Yehova? Afanana ndi inu ndani, wolemekezedwa, woyera, woopsa pomyamika, wakuchita zozizwa?” (Eksodo 15:11) Mawu otero abwerezedwa m’zaka mazana ambiri zonse kuyambira pamenepo. M’buku lomalizira la Baibulo, mtumwi Yohane akufotokoza kagulu ka atumiki okhulupirika odzozedwa a Mulungu: “Aimba nyimbo ya Mose kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa.” Kodi nyimbo yaikuluyi ndiyo iti? “Ntchito zanu nzazikulu ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse; njira zanu nzolungama ndi zoona, Mfumu inu ya nthaŵi zosatha. Ndani adzakhala wosawopa ndi wosalemekeza dzina lanu Ambuye? Chifukwa inu nokha muli woyera.”​—Chivumbulutso 15:2-4.

16, 17. Kodi nzochitika zodabwitsa zotani zimene tikuona zikuchitika lerolino?

16 Motero lerolinonso pali alambiri omasulidwa amene amayamikira ntchito za Mulungu ndi malamulo ake omwe. Anthu ochokera m’mitundu yonse amasulidwa mwauzimu, apatutsidwa ku dzikoli loipitsidwa chifukwa amadziŵa malamulo olungama a Mulungu ndi kuwachita. Chaka chilichonse, zikwi mazana a anthu amathaŵa dziko loipali kukakhala ndi gulu loyera, lolungama la alambiri a Yehova. Posachedwapa, pambuyo pa kuperekedwa kwa ziweruzo za Mulungu zamoto pa chipembedzo chonyenga ndi dongosolo loipali, iwo adzakhala ndi moyo kosatha m’dziko latsopano lolungama.

17 Mogwirizana ndi Chivumbulutso 14:6, 7, anthu tsopano akumva uthenga wochenjeza za chiweruzo wolalikidwa ndi Mboni za Yehova pansi pa chitsogozo cha angelo. M’maiko oposa 230 chaka chatha, Mboni pafupifupi mamiliyoni asanu zinalalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi ola lake la chiweruzo. Kuti aphunzitse anthu anzawo kuti akapulumuke, Mboni zinapanga maulendo obwerezabwereza kunyumba za anthu, kuchititsa maphunziro a Baibulo aulere. Motero zikwi mazana chaka chilichonse amaphunzira mokwana kuwopa Mulungu woona mwanzeru, kupatulira moyo wawo kwa iye, ndi kubatizidwa. Nkokondweretsa chotani nanga kuti anthu otere ayamba kuwopa Mulungu woona!​—Luka 1:49-51; Machitidwe 9:31; yerekezerani ndi Ahebri 11:7.

18. Kodi nchiyani chikusonyeza kuti angelo ali ndi mbali m’ntchito yathu yolalikira?

18 Kodi nzoona kuti angelo ali ndi mbali m’ntchito imeneyi ya kulalikira? Chabwino, nkwachionekera kuti nthaŵi zambiri angelo atsogolera Mboni za Yehova kunyumba kumene munthu wopsinjika mtima akufunadi, ngakhale kupempherera, thandizo lauzimu! Mwachitsanzo, Mboni za Yehova zina ziŵiri zotsagana ndi mwana wamng’ono zinali kulalikira uthenga wabwino pa chisumbu china cha ku Carribbean. Pamene kunakhala madzulo, achikulire aŵiriwo anafuna kuŵeruka. Koma mwanayo anali wofunitsitsa kwambiri kufikanso panyumba yotsatira. Pamene anaona kuti achikulire sanali ofunitsitsa kuchita motero panthaŵiyo, anapita yekha ndi kugogoda pa chitseko. Mkazi wachichepere anatsegula chitseko. Pamene achikulirewo anaona zimenezi, anapita kukalankhula naye. Anawaloŵetsa m’nyumba, ndi kufotokoza kuti panthaŵi imene anamva kugogoda pa chitseko, anali kupemphera kuti Mulungu amtumizire Mboni kuti zidzamphunzitse Baibulo. Makonzedwe a phunziro la Baibulo anapangidwa.

19. Kodi tingaloze ku chiyani monga phindu la kuwopa Mulungu?

19 Pamene tipereka uthenga wa chiweruzo cha Mulungu mokhulupirika, timaphunzitsanso malamulo ake olungama. Pamene izi zigwiritsiridwa ntchito m’moyo wa anthu, pamakhala madalitso akuthupi ndi akuuzimu. Mwachitsanzo, Baibulo nlomvekera bwino pa kutsutsa kwake chisembwere. (Aroma 1:26, 27, 32) Lerolino ambiri m’dziko lapansi amanyalanyaza miyezo yaumulungu. Kodi chotulukapo chake nchiyani? Maukwati akusweka. Kuswa malamulo kukufala. Matenda opatsirana mwa kugonana olemaza ndi akupha, amene akhala mliri m’zaka za zana lino la 20, akuwanda. Indedi, matenda owopsa a AIDS akufalikira kwakukulukulu mwa chisembwere. Koma kodi mantha aulemu kwa Mulungu sanakhale chitetezo chachikulu kwa alambiri oona?​—2 Akorinto 7:1; Afilipi 2:12; onaninso Machitidwe 15:28, 29.

Zotulukapo za Kuwopa Mulungu Tsopano

20. Kodi nchiyani chimasonyeza kuti ena amadziŵa za mbiri ya Mboni za Yehova?

20 Madalitso ngochuluka kwa awo amene amawopa Mulungu ndi kutsatira malamulo ake. Talingalirani za chochitika china chimene chimasonyeza kudziŵika komakula kwa kuti Mboni za Yehova zimapanga ubale wa mtendere wa Akristu a makhalidwe abwino. Mboni zingapo, nthumwi ku msonkhano wa mitundu yonse ku South America, zinali kukhala pa hotela imenenso kwa usiku umodzi inagwiritsiridwa ntchito ndi osakhala Mboni pamsonkhano wawo wodzatsogozedwa ndi pulezidenti wa dzikolo. Pamene gulu la alonda linafulumiza kuloŵa m’chikepe ndi pulezidenti, Mboni imene sinadziŵe amene anali m’chikepemo inaloŵanso momwemo, ikumadabwitsa alondawo! Itazindikira zimene inachita, Mboni yachikaziyo inapepesa kaamba ka msokonezowo. Inasonyeza baji lake la msonkhano wachigawo loidziŵikitsa kukhala Mboni ninena kuti sinafune konse kuvulaza pulezidenti. Akumwetulira, mlonda wina anati: “Bwenzi anthu onse akanakhala ngati Mboni za Yehova, sitikanafunikira chitetezo chotere.”​—Yesaya 2:2-4.

21. Kodi ndi zinthu zotani lerolino zimene anthu ayenera kuchita?

21 Umenewu ndiwo mtundu wa anthu amene Yehova akusonkhanitsa ndi kukonzekeretsa kuti ‘atuluke m’chisautso chachikulu’ chimene chidzathetsa dongosolo ili la zinthu. (Chivumbulutso 7:9, 10, 14) Kupulumukaku sikudzakhala kwa mwamwaŵi. Kuti munthu apulumuke, ayenera kuwopa Yehova, kumzindikira monga Mfumu yoyenera, ndi kudzipatulira kwa iye. Komabe, choonadi nchakuti, ambiri sadzakhala ndi mantha amene adzawadzetsera chitetezo. (Salmo 2:1-6) Malinga ndi maumboni onse amene alipo, Wolamulira wosankhidwa wa Yehova, Yesu Kristu, wakhala akulamulira monga Mfumu kuyambira chaka chofunikacho cha 1914. Izi zikutanthauza kuti nthaŵi yotsalayo ili kutha msanga kuti anthu akhale ndi mantha abwino kwa Yehova. Ngakhale zili tero, Mlengi wathu akulola anthu, ngakhale a malo apamwamba, kuyankha: “Tsono, mafumu inu, chitani mwanzeru: langikani, oweruza inu a dziko lapansi. Tumikirani Yehova ndi mantha, ndipo kondwerani ndi chinthenthe. Mpsompsoneni Mwanayo, kuti Angakwiye, ndipo mungatayike m’njira, ukayaka pang’ono pokha mkwiyo wake. Odala onse akumkhulupirira iye.”​—Salmo 2:7-12.

22. Kodi awo amene amawopa Mulungu tsopano ali ndi mtsogolo motani?

22 Tikhaletu pakati pa awo amene adzatamanda Mlengi wathu monga Uyo amene anatipulumutsa. Komabe, zimenezi zimafuna kuti ife tiwope Mulungu woona tsopano! (Yerekezerani ndi Salmo 2:11; Ahebri 12:28; 1 Petro 1:17.) Tiyenera kupitirizabe kuphunzira malamulo ake olungama ndi kuwalabadira. Nyimbo ya Mose ndi ya Mwanawankhosa, yolembedwa pa Chivumbulutso 15:3, 4, idzafika pachimake pamene Yehova adzachotsapo kuipa konse pa dziko lapansi ndi kuyamba kuchiritsa munthu ndi mudzi wake wa dziko lapansi pa zotulukapo za kuipitsa kwa uchimo. Ndiyeno, ndi mtima wathu wonse, tidzaimba kuti: “Ntchito zanu nzazikulu ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse; njira zanu nzolungama ndi zoona, Mfumu inu ya nthaŵi zosatha. Ndani adzakhala wosawopa ndi wosalemekeza dzina lanu Ambuye?”

Kodi Mukukumbukira?

◻ Kodi nchifukwa ninji Yehova ayenera mantha athu abwino?

◻ Kodi nchiyani chinasonyezedwa ndi zochita za Mulungu pa Nyanja Yofiira?

◻ Kodi ndi mapindu otani omwe kuwopa Yehova mwaulemu kumatipatsa?

◻ Kodi pali mtsogolo motani kwa awo amene amawopa Mulungu woona tsopano?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena