8 Choncho Yezebeli analemba makalata+ m’dzina la Ahabu n’kuwadinda ndi chidindo cha Ahabu.+ Kenako anatumiza makalatawo kwa akulu+ ndi anthu olemekezeka amene anali kukhala mumzinda umodzi ndi Naboti.
8 Ndiye inu lembani makalata m’malo mwa Ayuda. Mulembe zimene mukuona kuti n’zabwino kwa inu m’dzina la mfumu.+ Mudinde makalatawo ndi mphete yodindira ya mfumu, pakuti n’zosatheka kufafaniza makalata amene alembedwa m’dzina la mfumu ndi kudindidwa ndi mphete yake yodindira.”+