12 “Ukamachita kalembera pa ana a Isiraeli, + aliyense wa iwo azipereka dipo la moyo wake kwa Yehova pa nthawi yowawerengayo,+ kuti mliri usawagwere pochita kalemberayo.+
2 “Uwerenge+ khamu lonse la ana a Isiraeli malinga ndi mabanja awo, potsata nyumba za makolo awo, n’kulemba mayina awo. Uwerenge amuna onse, mmodzi ndi mmodzi.