19 inuyo simunawasiye m’chipululu chifukwa cha chifundo chanu chachikulu.+ Mtambo woima njo ngati chipilala sunawachokere usana ndipo unali kuwatsogolera,+ ngakhalenso moto woima njo ngati chipilala sunawachokere usiku ndipo unali kuwaunikira njira imene anayenera kuyendamo.+