22 Koma Hana sanapite nawo,+ pakuti anali atauza mwamuna wake kuti: “Mwanayu akangosiya kuyamwa,+ ndiyenera kupita naye kuti akaonekere pamaso pa Yehova ndi kukhala kumeneko mpaka kalekale.”*+
24 Mwanayo atangosiya kuyamwa, Hana anapita naye ku Silo atatenga ng’ombe yaing’ono yamphongo yazaka zitatu, ufa wokwana muyezo umodzi wa efa* ndi mtsuko waukulu wa vinyo.+ Iye analowa m’nyumba ya Yehova ku Silo,+ ndipo mwanayo anali naye limodzi.