-
1 Samueli 20:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Koma poyankha Davide analumbira+ kuti: “Bambo ako ayenera kuti akudziwa ndithu kuti iweyo umandikonda.+ Pa chifukwa chimenechi iwo adzanena kuti, ‘Musamuuze zimenezi Yonatani kuti zingamupweteketse mtima.’ Moti ndikunenetsa, pali Yehova Mulungu wamoyo,+ komanso pali moyo wako,+ imfa ili pafupi kwambiri ndi ine!”+
-
-
2 Samueli 11:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Pamenepo Uriya anayankha Davide kuti: “Likasa,+ Isiraeli ndi Yuda akukhala m’misasa, ndipo mbuyanga Yowabu pamodzi ndi atumiki anu mbuyanga+ ali mumsasa kuthengo. Ndiye ine ndikalowe m’nyumba yanga kukadya chakudya, kumwa ndi kugona ndi mkazi wanga?+ Ndithu, pali inu ndi moyo wanu,+ sindingachite zimenezo.”
-