Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Samueli 18:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Tsopano Abisalomu akali moyo anadzimangira chipilala.+ Chipilala chimenechi chili m’Chigwa cha Mfumu,+ pakuti iye anati: “Ine ndilibe mwana wamwamuna woti asunge dzina langa monga chikumbukiro.”+ Choncho chipilala chimenecho anachitcha dzina lake+ ndipo chikudziwikabe ndi dzina lakuti Chipilala cha Abisalomu kufikira lero.

  • Salimo 49:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Zokhumba za mtima wawo n’zakuti nyumba zawo zikhalebe mpaka kalekale,+

      Mahema awo akhalebe ku mibadwomibadwo.+

      Malo awo amawatcha mayina awo.+

  • Miyambo 8:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Kuopa Yehova kumatanthauza kudana ndi zoipa.+ Ndimadana ndi kudzikweza, kunyada,+ njira yoipa ndiponso pakamwa ponena zopotoka.+

  • Miyambo 15:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Yehova adzagwetsa nyumba za anthu odzikuza,+ koma adzakhazikitsa malire a malo a mkazi wamasiye.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena