32 M’kupita kwa nthawi, Gidiyoni mwana wa Yowasi anamwalira ali wokalamba, atakhala ndi moyo wabwino ndi wautali, ndipo anamuika m’manda a Yowasi bambo ake, mumzinda wa Ofira wa Aabi-ezeri.+
31 Kenako abale ake ndi anthu onse a m’nyumba ya bambo ake, anapita kumeneko kukatenga mtembo wa Samisoni ndi kubwera nawo kwawo, ndipo anamuika m’manda a bambo ake Manowa,+ pakati pa Zora+ ndi Esitaoli.+ Samisoni anali ataweruza Isiraeli zaka 20.+