16 Zimene wachitazi si zabwino ayi. Pali Yehova, Mulungu wamoyo,+ anthu inu muyenera kufa ndithu,+ chifukwa simunayang’anire+ mbuye wanu. Ndithu simunayang’anire wodzozedwa wa Yehova.+ Tsopano taonani kumene kuli mkondo wa mfumu ndi mtsuko wake wa madzi+ zimene zinali chakumutu kwake.”