2 Samueli 11:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Kenako Davide anatuma nthumwi kuti akamutenge.+ Choncho mkaziyo anabweradi kwa Davide+ ndipo Davide anagona naye+ pa nthawi imene mkaziyo anali kudziyeretsa ku chodetsa chake.+ Zitatero mkaziyo anabwerera kunyumba yake. 2 Samueli 11:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Pamapeto pake, Davide anauza Uriya kuti: “Pita kunyumba kwako ukasambe mapazi ako.”+ Uriya anatuluka m’nyumba ya mfumu ndipo pambuyo pake mfumuyo inamutumizira mphatso. 2 Samueli 11:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Kuwonjezera apo, Davide anamuitana kuti adye ndi kumwa naye pamodzi, ndipo anamuledzeretsa.+ Ngakhale zinali choncho, madzulo Uriya anapita kwa atumiki a mbuye wake kukagona pabedi, ndipo sanapite kunyumba kwake. 2 Samueli 11:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 M’kalatamo analembamo kuti:+ “Muike Uriya kutsogolo kumene nkhondo yakula,+ ndipo inu mubwerere m’mbuyo kuti amukanthe ndipo afe ndithu.”+
4 Kenako Davide anatuma nthumwi kuti akamutenge.+ Choncho mkaziyo anabweradi kwa Davide+ ndipo Davide anagona naye+ pa nthawi imene mkaziyo anali kudziyeretsa ku chodetsa chake.+ Zitatero mkaziyo anabwerera kunyumba yake.
8 Pamapeto pake, Davide anauza Uriya kuti: “Pita kunyumba kwako ukasambe mapazi ako.”+ Uriya anatuluka m’nyumba ya mfumu ndipo pambuyo pake mfumuyo inamutumizira mphatso.
13 Kuwonjezera apo, Davide anamuitana kuti adye ndi kumwa naye pamodzi, ndipo anamuledzeretsa.+ Ngakhale zinali choncho, madzulo Uriya anapita kwa atumiki a mbuye wake kukagona pabedi, ndipo sanapite kunyumba kwake.
15 M’kalatamo analembamo kuti:+ “Muike Uriya kutsogolo kumene nkhondo yakula,+ ndipo inu mubwerere m’mbuyo kuti amukanthe ndipo afe ndithu.”+