2 Koma Davide anatenga chisoti chachifumu chimene chinali kumutu kwa Malikamu,+ ndipo golide wa chisoticho anali wolemera talente limodzi. Chisoticho chinalinso ndi miyala yamtengo wapatali. Kenako anthu anaveka Davide chisoticho. Zinthu zimene anafunkha mumzindawo zinali zochuluka kwambiri.+