30 Iye analanda chisoti chachifumu chimene chinali kumutu kwa Malikamu,+ ndipo anthu anaveka Davide chisoticho. Golide wa chisoticho anali wolemera talente limodzi, ndipo chisoticho chinalinso ndi miyala yamtengo wapatali. Zinthu zimene anafunkha+ mumzindawo zinali zochuluka kwambiri.