Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 13:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 “M’bale wako, amene ndi mwana wamwamuna wa mayi ako, kapena mwana wako wamwamuna, mwana wako wamkazi, mkazi wako wokondedwa kapena bwenzi lako lapamtima,+ akayesa kukupatutsa mwamseri pokuuza kuti, ‘Tiye tikatumikire milungu ina,’+ milungu imene iwe kapena makolo ako sanaidziwe,

  • 2 Mbiri 15:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Mfumu Asa+ inachotsa ngakhalenso agogo ake aakazi a Maaka+ pa udindo wawo wokhala mayi wa mfumu,+ chifukwa anapanga fano lonyansa kwambiri+ lopembedzera mzati wopatulika.+ Kenako Asa anagwetsa fanolo ndipo analiperapera n’kukalitentha+ m’chigwa cha Kidironi.+

  • Zekariya 13:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Pakadzapezeka munthu aliyense wolosera, bambo ake ndi mayi ake amene anamubereka, adzamuuze kuti, ‘Iwe ufa ndithu, chifukwa walankhula zonama m’dzina la Yehova.’ Ndiyeno bambo ndi mayi akewo adzamulase chifukwa chakuti anali kulosera.+

  • Mateyu 10:37
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 37 Amene amakonda kwambiri bambo ake kapena mayi ake kuposa ine sali woyenera ine. Komanso amene amakonda kwambiri mwana wake wamwamuna kapena wamkazi kuposa ine sali woyenera ine.+

  • Luka 12:53
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 53 Iwo adzagawanika, bambo kutsutsana ndi mwana wake wamwamuna, ndipo mwana wamwamuna kutsutsana ndi bambo ake. Mayi kutsutsana ndi mwana wake wamkazi, ndipo mwana wamkazi kutsutsana ndi mayi ake. Mpongozi kutsutsana ndi mkazi wa mwana wake, ndipo mkazi wokwatiwa kutsutsana ndi apongozi ake aakazi.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena