-
2 Mafumu 17:13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Yehova anali kuchenjeza+ Aisiraeli+ ndi Ayuda+ kudzera mwa aneneri ake onse+ ndi wamasomphenya aliyense,+ kuti: “Siyani njira zanu zoipa+ ndipo sungani malamulo anga,+ mogwirizana ndi chilamulo chonse+ chimene ndinalamula makolo anu,+ ndi chimene ndinakutumizirani kudzera mwa atumiki anga, aneneri.”+
-
-
Yeremiya 11:4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Makolo anu ndinawalamula kumvera mawu amenewa pamene ndinali kuwatulutsa m’dziko la Iguputo,+ pamene ndinali kuwatulutsa m’ng’anjo yachitsulo.+ Ndinawalamula kuti, ‘Muzimvera mawu anga, ndipo muzichita zinthu motsatira malamulo onse amene ndakupatsani.+ Mukatero mudzakhaladi anthu anga, ndipo ine ndidzakhala Mulungu wanu,+
-