21 Mfumu Uziya+ inakhalabe yakhate mpaka tsiku limene inamwalira. Iyo inali kungokhala m’nyumba ina chifukwa cha khatelo+ osagwiranso ntchito, popeza inali itachotsedwa m’nyumba ya Yehova. Pa nthawiyi, Yotamu mwana wake ndiye anali kuyang’anira nyumba ya mfumu ndi kuweruza anthu a m’dzikolo.