Levitiko 13:46 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 46 Masiku onse pamene akudwala nthendayo azikhala wodetsedwa. Iye ndi wodetsedwa ndipo azikhala payekha. Azikhala kunja kwa msasa.+ Numeri 5:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 “Lamula ana a Isiraeli kuti azitulutsa mumsasa munthu aliyense wakhate,+ aliyense wakukha kumaliseche,+ ndi aliyense wodetsedwa chifukwa chokhudza mtembo wa munthu.+ Numeri 12:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Kodi bambo ake akanam’lavulira+ malovu kumaso, sakanakhala wonyazitsidwa masiku 7? Choncho m’tulutseni+ akakhale kunja kwa msasa masiku 7,+ pambuyo pake mum’landire mumsasamo.”+ Numeri 12:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Chotero Miriamu anatulutsidwa kukakhala kunja kwa msasa masiku 7,+ ndipo anthuwo sanasamuke kufikira Miriamu atalandiridwanso mumsasa. 2 Mafumu 7:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Ndiyeno panali anthu anayi akhate amene anali pachipata.+ Iwo anayamba kufunsana kuti: “Kodi tikhalirenji pano mpaka kufa?
46 Masiku onse pamene akudwala nthendayo azikhala wodetsedwa. Iye ndi wodetsedwa ndipo azikhala payekha. Azikhala kunja kwa msasa.+
2 “Lamula ana a Isiraeli kuti azitulutsa mumsasa munthu aliyense wakhate,+ aliyense wakukha kumaliseche,+ ndi aliyense wodetsedwa chifukwa chokhudza mtembo wa munthu.+
14 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Kodi bambo ake akanam’lavulira+ malovu kumaso, sakanakhala wonyazitsidwa masiku 7? Choncho m’tulutseni+ akakhale kunja kwa msasa masiku 7,+ pambuyo pake mum’landire mumsasamo.”+
15 Chotero Miriamu anatulutsidwa kukakhala kunja kwa msasa masiku 7,+ ndipo anthuwo sanasamuke kufikira Miriamu atalandiridwanso mumsasa.
3 Ndiyeno panali anthu anayi akhate amene anali pachipata.+ Iwo anayamba kufunsana kuti: “Kodi tikhalirenji pano mpaka kufa?