21 Ndiyeno Arauna anafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani inu mbuyanga mfumu mwabwera kwa ine mtumiki wanu?” Poyankha Davide anati: “Ndabwera kuti undigulitse+ malo ako opunthira mbewu. Ndikufuna kumangira Yehova guwa lansembe pamenepo, kuti mliriwu+ uthe pakati pa anthuwa.”