16 Koma atangokhala wamphamvu, mtima wake unadzikuza+ mpaka kufika pom’pweteketsa.+ Choncho anachita zosakhulupirika kwa Yehova Mulungu wake ndipo anapita m’kachisi wa Yehova kukafukiza paguwa lansembe zofukiza.+
25 Koma Hezekiya sanabwezere zabwino zimene anachitiridwa,+ pakuti mtima wake unayamba kudzikuza+ ndipo mkwiyo wa Mulungu+ unayakira iyeyo, Yuda, ndi Yerusalemu.
20 Koma pamene mtima wake unayamba kudzitukumula ndiponso pamene anaumitsa mtima wake ndi kuchita zinthu modzikweza,+ anatsitsidwa pampando wake wachifumu ndipo ulemerero wake unachotsedwa.+