Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mafumu 23:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Kenako mfumuyo inalamula Hilikiya+ mkulu wa ansembe, ansembe ena, ndi alonda a pakhomo+ kuti atulutse m’kachisi wa Yehova ziwiya zonse zimene anapangira Baala,+ mzati wopatulika,+ ndi khamu lonse la zinthu zakuthambo.+ Itatero, inakazitentha kunja kwa Yerusalemu pamalo otsetsereka a ku Kidironi,+ ndipo inabweretsa phulusa lake ku Beteli.+

  • 2 Mafumu 23:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Kuwonjezera apo, mfumuyo inatulutsa mzati wopatulika+ umene unali m’nyumba ya Yehova, ndipo inapita nawo kuchigwa* cha Kidironi kunja kwa mzinda wa Yerusalemu n’kukautentha+ kuchigwacho. Itatero, inauperapera n’kuwaza fumbi lake pamanda+ a ana a anthu.

  • 2 Mbiri 15:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Mfumu Asa+ inachotsa ngakhalenso agogo ake aakazi a Maaka+ pa udindo wawo wokhala mayi wa mfumu,+ chifukwa anapanga fano lonyansa kwambiri+ lopembedzera mzati wopatulika.+ Kenako Asa anagwetsa fanolo ndipo analiperapera n’kukalitentha+ m’chigwa cha Kidironi.+

  • Yohane 18:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Atanena zimenezi, Yesu anatuluka pamodzi ndi ophunzira ake ndi kuwoloka khwawa la Kidironi,+ kupita kumene kunali munda. Ndipo iye ndi ophunzira akewo analowa m’mundamo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena