2 Iwo alola ena mwa ana aakazi a mitundu inayo kuti akhale akazi awo ndi akazi a ana awo aamuna,+ ndipo iwo omwe ndi mtundu wopatulika,+ asakanikirana+ ndi anthu a mitundu ina. Akalonga ndi atsogoleri ndiwo ali patsogolo+ pa kusakhulupirika kumeneku.”
28 Ndiyeno mmodzi mwa ana aamuna a Yoyada,+ mwana wa Eliyasibu,+ mkulu wa ansembe anali mkamwini wa Sanibalati+ wa ku Beti-horoni.+ Choncho ndinamuthamangitsa, kum’chotsa pamaso panga.+