-
Esitere 3:13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Ndiyeno anatumiza makalatawo kudzera mwa amtokoma+ kupita kuzigawo zonse za mfumu. Anachita izi kuti pa tsiku limodzi,+ pa tsiku la 13 la mwezi wa 12 umene ndi mwezi wa Adara,+ awononge, aphe ndi kufafaniza Ayuda onse, mnyamata komanso mwamuna wachikulire, ana ndi akazi ndi kufunkha zinthu zawo.+
-
-
Esitere 9:1Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Tsiku la 13 la mwezi wa 12, umene ndi mwezi wa Adara,*+ linali tsiku limene mawu a mfumu ndi chilamulo chake zinayenera kuchitika.+ Limeneli linali tsiku limene adani a Ayuda anali kuyembekezera kugonjetsa Ayudawo. Koma pa tsikuli zinthu zinasintha, moti Ayudawo ndi amene anagonjetsa anthu amene anali kudana nawo.+
-