Yobu 31:35 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 35 Ndikulakalaka ndikanakhala ndi wina wondimvetsera,+Kuti mogwirizana ndi chizindikiro changa chochita kulemba, Wamphamvuyonse andiyankhe.+Ndikulakalaka munthu amene ali nane pa mlandu akanalemba chikalata. Mlaliki 6:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Chilichonse chimene chinakhalapo chinapatsidwa kale dzina, ndipo zinadziwika kale kuti munthu ndi ndani.+ Iye sangathe kudziteteza pa mlandu wotsutsana ndi amene ali wamphamvu kuposa iyeyo.+ Yesaya 45:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Tsoka kwa amene walimbana ndi amene anamuumba,+ ngati phale limene likulimbana ndi mapale ena amene ali pansi. Kodi dongo+ lingafunse amene akuliumba kuti: “Kodi ukupanga chiyani?” Ndipo kodi chimene unapanga chinganene kuti: “Amene uja alibe manja”? Aroma 9:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Munthu iwe!+ Iweyo ndiwe ndani kuti uziyankhana ndi Mulungu?+ Kodi chinthu choumbidwa chinganene kwa munthu amene anachiumba kuti, “Unandipangiranji motere?”+
35 Ndikulakalaka ndikanakhala ndi wina wondimvetsera,+Kuti mogwirizana ndi chizindikiro changa chochita kulemba, Wamphamvuyonse andiyankhe.+Ndikulakalaka munthu amene ali nane pa mlandu akanalemba chikalata.
10 Chilichonse chimene chinakhalapo chinapatsidwa kale dzina, ndipo zinadziwika kale kuti munthu ndi ndani.+ Iye sangathe kudziteteza pa mlandu wotsutsana ndi amene ali wamphamvu kuposa iyeyo.+
9 Tsoka kwa amene walimbana ndi amene anamuumba,+ ngati phale limene likulimbana ndi mapale ena amene ali pansi. Kodi dongo+ lingafunse amene akuliumba kuti: “Kodi ukupanga chiyani?” Ndipo kodi chimene unapanga chinganene kuti: “Amene uja alibe manja”?
20 Munthu iwe!+ Iweyo ndiwe ndani kuti uziyankhana ndi Mulungu?+ Kodi chinthu choumbidwa chinganene kwa munthu amene anachiumba kuti, “Unandipangiranji motere?”+