Mateyu 24:38 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 38 M’masiku amenewo chigumula chisanafike, anthu anali kudya ndi kumwa. Amuna anali kukwatira ndipo akazi anali kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa+ analowa m’chingalawa.+ Luka 12:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Koma Mulungu anamuuza kuti, ‘Wopanda nzeru iwe, usiku womwe uno moyo wako adzaufuna.+ Nanga chuma chimene waunjikachi chidzakhala cha ndani?’+ Luka 17:28 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 28 Chimodzimodzinso ndi zimene zinachitika m’masiku a Loti.+ M’masiku amenewo anthu anali kudya, kumwa, kugula, kugulitsa, kubzala ndi kumanga. 1 Akorinto 15:32 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 32 Ngati ndinamenyana ndi zilombo ku Efeso+ monga ena anachitira, ndinapindulapo chiyani? Ngati akufa sadzauka, “tiyeni tidye ndi kumwa, pakuti mawa tifa.”+
38 M’masiku amenewo chigumula chisanafike, anthu anali kudya ndi kumwa. Amuna anali kukwatira ndipo akazi anali kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa+ analowa m’chingalawa.+
20 Koma Mulungu anamuuza kuti, ‘Wopanda nzeru iwe, usiku womwe uno moyo wako adzaufuna.+ Nanga chuma chimene waunjikachi chidzakhala cha ndani?’+
28 Chimodzimodzinso ndi zimene zinachitika m’masiku a Loti.+ M’masiku amenewo anthu anali kudya, kumwa, kugula, kugulitsa, kubzala ndi kumanga.
32 Ngati ndinamenyana ndi zilombo ku Efeso+ monga ena anachitira, ndinapindulapo chiyani? Ngati akufa sadzauka, “tiyeni tidye ndi kumwa, pakuti mawa tifa.”+