Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Numeri 15:39
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 39 ‘Chingwecho chikhale ngati mphonje kwa inu, kuti mukachiyang’ana muzikumbukira malamulo onse+ a Yehova ndi kuwasunga. Muleke kutsatira zilakolako za mitima yanu ndi maso anu,+ chifukwa potsatira zilakolako zimenezo, mukuchita chiwerewere.+

  • Mlaliki 11:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Mnyamatawe, sangalala+ ndi unyamata wako, ndipo mtima wako ukusangalatse masiku a unyamata wako. Yenda m’njira za mtima wako ndiponso motsatira zimene maso ako akuona.+ Koma dziwa kuti Mulungu woona adzakuweruza chifukwa cha zonsezi.+

  • Ezekieli 6:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Opulumuka anu akadzagwidwa n’kutengedwa kukakhala pakati pa mitundu ina ya anthu, ndithu adzandikumbukira.+ Adzakumbukira mmene ndinamvera kupweteka chifukwa cha mtima wawo wadama umene unawachititsa kundipandukira.+ Adzakumbukiranso mmene ndinamvera kupweteka chifukwa cha maso awo othamangira mafano awo onyansa pofuna kuchita nawo zadama.+ Iwo adzachita manyazi ochita kuonekera pankhope zawo, chifukwa cha zinthu zonse zoipa ndi zonyansa zimene anachita.+

  • Mateyu 5:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Tsopano ngati diso lako lakumanja limakuchimwitsa,* ulikolowole ndi kulitaya.+ Pakuti n’kwabwino kuti ukhale wopanda chiwalo chimodzi kusiyana n’kuti thupi lako lonse lidzaponyedwe+ m’Gehena.

  • 1 Yohane 2:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Pakuti chilichonse cha m’dziko,+ monga chilakolako cha thupi,+ chilakolako cha maso+ ndi kudzionetsera ndi zimene munthu ali nazo pa moyo wake,+ sizichokera kwa Atate, koma kudziko.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena