Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 32:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Iye ndi Thanthwe, ndipo ntchito yake ndi yangwiro,+

      Njira zake zonse ndi zolungama.+

      Mulungu wokhulupirika,+ amene sachita chosalungama.+

      Iye ndi wolungama ndi wowongoka.+

  • Salimo 11:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  7 Pakuti Yehova ndi wolungama.+ Amakonda ntchito zolungama.+

      Anthu owongoka mtima ndi amene adzaona nkhope yake.+

  • Salimo 139:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Ndidzakutamandani chifukwa munandipanga modabwitsa ndipo zimenezi zimandichititsa mantha.+

      Ntchito zanu ndi zodabwitsa,+

      Ndipo ine ndimadziwa bwino zimenezi.+

  • Salimo 139:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Maso anu anandiona pamene ndinali mluza,+

      Ndipo ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’buku lanu.

      M’bukumo munalembamo za masiku amene zinapangidwa+

      Koma panalibe ngakhale chiwalo chimodzi chimene chinali chitapangidwa.

  • Danieli 9:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 “Inu Yehova, munakhala tcheru kuti mutigwetsere tsoka ndipo pamapeto pake munatigwetseradi tsokalo,+ pakuti inu Yehova Mulungu wathu ndinu wolungama pa ntchito zanu zonse zimene mwachita, koma ife sitinamvere mawu anu.+

  • Chivumbulutso 15:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Iwo akuimba nyimbo ya Mose+ kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa,+ yakuti:

      “Ntchito zanu n’zazikulu ndi zodabwitsa,+ inu Yehova Mulungu Wamphamvuyonse.+ Njira zanu ndi zolungama ndi zoona,+ inu Mfumu yamuyaya.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena