Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Samueli 29:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Pamenepo akalonga a Afilisiti anam’psera mtima kwambiri Akisi, ndipo anati: “Muuze abwerere,+ apite kumalo amene unam’patsa. Usamulole kuti apite nafe kunkhondo chifukwa angakatitembenukire+ kumeneko. Ukuganiza kuti munthu ameneyu adzakometsera dzina lake ndi chiyani kwa mbuye wake? Si mitu ya asilikali athu kodi?

  • 2 Samueli 19:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Koma Davide anati: “Ndili nanu chiyani+ inu ana a Zeruya kuti lero mukhale otsutsana+ nane? Kodi mu Isiraeli muyenera kuphedwa munthu aliyense lero?+ Kodi ine sindikudziwa bwino kuti lero ndine mfumu ya Isiraeli?”

  • 1 Mafumu 11:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Kenako Yehova anasankha munthu woti azilimbana+ ndi Solomo.+ Munthuyo dzina lake linali Hadadi, Mwedomu, mbadwa ya mfumu, ndipo anali kukhala ku Edomu.+

  • Zekariya 3:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Ndiyeno Mulungu anandionetsa Yoswa+ mkulu wa ansembe, ataimirira pamaso pa mngelo wa Yehova. Pa nthawiyi Satana+ anali ataimirira kudzanja lamanja la Yoswa kuti azim’tsutsa.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena