2 Samueli 7:28 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 28 Tsopano inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, ndinu Mulungu woona. Kunena za mawu anu, akhale oona,+ pakuti mwandilonjeza ine mtumiki wanu zabwino zimenezi.+ 1 Mafumu 17:24 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 24 Mayiyo ataona zimenezi anauza Eliya kuti: “Tsopano ndadziwadi kuti ndinu munthu wa Mulungu+ ndipo mawu a Yehova amene ali m’kamwa mwanu ndi oona.”+ Salimo 12:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Mawu a Yehova ndi oyengeka bwino,+Ngati siliva woyengedwa nthawi zokwanira 7 mung’anjo ya m’nthaka. Salimo 119:140 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 140 Mawu anu ndi oyengeka kwambiri,+Ndipo ine mtumiki wanu ndimawakonda.+ Miyambo 30:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Mawu alionse a Mulungu ndi oyera.+ Iye ndi chishango kwa onse othawira kwa iye.+ Yohane 17:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Ayeretseni+ ndi choonadi. Mawu+ anu ndiwo choonadi.+
28 Tsopano inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, ndinu Mulungu woona. Kunena za mawu anu, akhale oona,+ pakuti mwandilonjeza ine mtumiki wanu zabwino zimenezi.+
24 Mayiyo ataona zimenezi anauza Eliya kuti: “Tsopano ndadziwadi kuti ndinu munthu wa Mulungu+ ndipo mawu a Yehova amene ali m’kamwa mwanu ndi oona.”+
6 Mawu a Yehova ndi oyengeka bwino,+Ngati siliva woyengedwa nthawi zokwanira 7 mung’anjo ya m’nthaka.