Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Samueli 25:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Nthawi yomweyo, Abigayeli+ anafulumira kutenga mitanda 200 ya mkate, mitsuko iwiri ikuluikulu ya vinyo,+ anapha nkhosa zisanu,+ anatenganso miyezo ya seya* isanu ya tirigu wokazinga,+ mphesa zouma zoumba pamodzi 100+ ndi nkhuyu zouma zoumba pamodzi 200+ ndi kuzikweza pa abulu.

  • Miyambo 19:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Wokomera mtima munthu wonyozeka akukongoza Yehova,+ ndipo adzam’bwezera zimene anachitazo.+

  • Miyambo 22:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Wa diso labwino adzadalitsidwa, chifukwa amapereka chakudya chake kwa munthu wonyozeka.+

  • Machitidwe 9:36
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 36 Koma ku Yopa+ kunali wophunzira wina dzina lake Tabita, dzina limene polimasulira limatanthauza Dorika.* Tabita anali kuchita ntchito zabwino zambiri,+ ndi kupereka mphatso zachifundo zochuluka.

  • Aefeso 4:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Wakubayo asabenso,+ koma agwire ntchito molimbikira. Agwire ndi manja ake ntchito yabwino,+ kuti akhale ndi kanthu kena kopatsa munthu wosowa.+

  • 1 Timoteyo 2:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Koma azidzikongoletsa mogwirizana ndi mmene akazi amene amati amalemekeza Mulungu amayenera kudzikongoletsera.+ Azidzikongoletsa ndi ntchito zabwino.+

  • Aheberi 13:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Komanso, musaiwale kuchita zabwino+ ndi kugawana zinthu ndi ena, pakuti nsembe zotero Mulungu amakondwera nazo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena