Salimo 10:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Iye amabisalira anthu pafupi ndi midzi.Amabisalira munthu wosalakwa ndi kumupha.+ ע [ʽAʹyin]Maso ake amafunafuna waumphawi.+ Salimo 17:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Aliyense wa iwo akuoneka ngati mkango umene ukufunitsitsa kukhadzula nyama.+Akuonekanso ngati mkango wamphamvu umene wabisalira nyama. Salimo 56:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Amandiukira ndi kundibisalira,+Iwo nthawi zonse amaonetsetsa mmene ndikuyendera,+Pamene akundidikirira kuti awononge moyo wanga.+ Mateyu 26:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Iwo anali kupangana+ zoti agwire Yesu mochenjera ndi kumupha. Machitidwe 23:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Tsopano, inuyo pamodzi ndi Khoti Lalikulu la Ayuda, mufotokoze momveka bwino kwa mkulu wa asilikali. Mumuuze kuti amubweretse kwa inu, ngati kuti mukufuna kumvetsetsa bwino nkhani yokhudza munthu ameneyu.+ Koma asanafike n’komwe ife tidzakhala okonzeka kumupha.”+
8 Iye amabisalira anthu pafupi ndi midzi.Amabisalira munthu wosalakwa ndi kumupha.+ ע [ʽAʹyin]Maso ake amafunafuna waumphawi.+
12 Aliyense wa iwo akuoneka ngati mkango umene ukufunitsitsa kukhadzula nyama.+Akuonekanso ngati mkango wamphamvu umene wabisalira nyama.
6 Amandiukira ndi kundibisalira,+Iwo nthawi zonse amaonetsetsa mmene ndikuyendera,+Pamene akundidikirira kuti awononge moyo wanga.+
15 Tsopano, inuyo pamodzi ndi Khoti Lalikulu la Ayuda, mufotokoze momveka bwino kwa mkulu wa asilikali. Mumuuze kuti amubweretse kwa inu, ngati kuti mukufuna kumvetsetsa bwino nkhani yokhudza munthu ameneyu.+ Koma asanafike n’komwe ife tidzakhala okonzeka kumupha.”+