26 Pamenepo Elisa anati: “Kodi mtima wanga sunali nawe limodzi pamene munthuyo anali kutembenuka ndi kutsika pagaleta lake kuti akumane nawe? Kodi ino ndi nthawi yolandira siliva, zovala, minda ya maolivi, minda ya mpesa, nkhosa, ng’ombe, antchito aamuna, kapena antchito aakazi?+