Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 15:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Pa nthawiyo Mose ndi ana a Isiraeli anayamba kuimbira Yehova nyimbo iyi, kuti:+

      “Ndiimbira Yehova, pakuti iye wakwezeka koposa.+

      Waponyera m’nyanja mahatchi ndi okwera pamahatchiwo.+

  • Deuteronomo 31:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 “Tsopano dzilembereni nyimbo iyi+ ndi kuwaphunzitsa ana a Isiraeli.+ Muiike m’kamwa mwawo kuti nyimbo imeneyi ikhale mboni yanga pamaso pa ana a Isiraeliwo.+

  • Oweruza 5:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Pa tsiku limenelo, Debora+ ndi Baraki+ mwana wa Abinowamu,+ anayamba kuimba nyimbo,+ ndipo anati:

  • 2 Samueli 22:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Davide analankhula ndi Yehova mawu a nyimbo iyi,+ pa tsiku limene Yehova anamulanditsa kwa adani ake+ onse ndiponso m’manja mwa Sauli.+

  • Salimo 18:kam
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la mtumiki wa Yehova, Davide, amene anauza Yehova mawu a m’nyimbo iyi pa tsiku limene Yehova anamulanditsa m’manja mwa adani ake onse komanso m’manja mwa Sauli.+ Iye anati:

  • Yesaya 5:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Ndikufuna ndimuimbire nyimbo munthu amene ndimamukonda. Imeneyi ndi nyimbo yonena za munthu amene ndimamukonda, ndiponso munda wake wa mpesa.+ Wokondedwa wanga anali ndi munda wa mpesa pamalo achonde m’mbali mwa phiri.

  • Chivumbulutso 15:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Iwo akuimba nyimbo ya Mose+ kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa,+ yakuti:

      “Ntchito zanu n’zazikulu ndi zodabwitsa,+ inu Yehova Mulungu Wamphamvuyonse.+ Njira zanu ndi zolungama ndi zoona,+ inu Mfumu yamuyaya.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena