Ekisodo 19:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Inuyo mudzakhala ufumu wanga wa ansembe ndi mtundu wanga woyera.’+ Ukanene mawu amenewa kwa ana a Isiraeli.” Deuteronomo 4:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Ndipo ndi mtundu winanso uti wamphamvu umene uli ndi malangizo ndi zigamulo zolungama zofanana ndi chilamulo chonsechi chimene ndikukuikirani pamaso panu lero?+ Malaki 3:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 “Iwo adzakhala anthu anga,+ pa tsiku limene ndidzawasandutse chuma chapadera,”+ watero Yehova wa makamu. “Ndidzawachitira chifundo monga mmene munthu amachitira chifundo mwana wake amene amamutumikira.+ Machitidwe 2:47 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 47 Anali kutamanda Mulungu ndipo anthu onse anali kuwakonda.+ Komanso tsiku ndi tsiku, Yehova anapitiriza kuwawonjezera+ anthu amene anali kuwapulumutsa.+ 1 Petulo 2:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Koma inu ndinu “fuko losankhidwa mwapadera, ansembe achifumu, mtundu woyera,+ anthu odzakhala chuma chapadera,+ kuti mulengeze makhalidwe abwino kwambiri”+ a amene anakuitanani kuchoka mu mdima kulowa m’kuwala kwake kodabwitsa.+
6 Inuyo mudzakhala ufumu wanga wa ansembe ndi mtundu wanga woyera.’+ Ukanene mawu amenewa kwa ana a Isiraeli.”
8 Ndipo ndi mtundu winanso uti wamphamvu umene uli ndi malangizo ndi zigamulo zolungama zofanana ndi chilamulo chonsechi chimene ndikukuikirani pamaso panu lero?+
17 “Iwo adzakhala anthu anga,+ pa tsiku limene ndidzawasandutse chuma chapadera,”+ watero Yehova wa makamu. “Ndidzawachitira chifundo monga mmene munthu amachitira chifundo mwana wake amene amamutumikira.+
47 Anali kutamanda Mulungu ndipo anthu onse anali kuwakonda.+ Komanso tsiku ndi tsiku, Yehova anapitiriza kuwawonjezera+ anthu amene anali kuwapulumutsa.+
9 Koma inu ndinu “fuko losankhidwa mwapadera, ansembe achifumu, mtundu woyera,+ anthu odzakhala chuma chapadera,+ kuti mulengeze makhalidwe abwino kwambiri”+ a amene anakuitanani kuchoka mu mdima kulowa m’kuwala kwake kodabwitsa.+