Ekisodo 20:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 “Usagwiritse ntchito dzina la Yehova Mulungu wako mosasamala,+ pakuti Yehova sadzalekerera aliyense wogwiritsa ntchito dzina lake mosasamala osam’langa.+ Yoswa 24:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 Ndiyeno Yoswa anauza anthuwo kuti: “Simungathe kutumikira Yehova, chifukwa iye ndi Mulungu woyera.+ Iye ndi Mulungu amene amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha.+ Iye sadzakhululuka machimo anu ndi kupanduka kwanu.+ Yeremiya 18:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Koma inu Yehova mukudziwa bwino chiwembu chimene andikonzera kuti andiphe.+ Musakhululukire* cholakwa chawo, ndipo musafafanize tchimo lawolo pamaso panu. Koma iwo apunthwe pamaso panu.+ Muwachitire zimenezi pa nthawi ya mkwiyo wanu.+ Maliko 3:29 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 29 Komabe, aliyense amene wanyoza mzimu woyera sadzakhululukidwa kwamuyaya, koma adzakhala ndi mlandu wa tchimo losatha.”+
7 “Usagwiritse ntchito dzina la Yehova Mulungu wako mosasamala,+ pakuti Yehova sadzalekerera aliyense wogwiritsa ntchito dzina lake mosasamala osam’langa.+
19 Ndiyeno Yoswa anauza anthuwo kuti: “Simungathe kutumikira Yehova, chifukwa iye ndi Mulungu woyera.+ Iye ndi Mulungu amene amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha.+ Iye sadzakhululuka machimo anu ndi kupanduka kwanu.+
23 Koma inu Yehova mukudziwa bwino chiwembu chimene andikonzera kuti andiphe.+ Musakhululukire* cholakwa chawo, ndipo musafafanize tchimo lawolo pamaso panu. Koma iwo apunthwe pamaso panu.+ Muwachitire zimenezi pa nthawi ya mkwiyo wanu.+
29 Komabe, aliyense amene wanyoza mzimu woyera sadzakhululukidwa kwamuyaya, koma adzakhala ndi mlandu wa tchimo losatha.”+