Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 6:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Iye anapitiriza kunena kuti: “Pita ukauze anthu awa kuti, ‘Imvani mobwerezabwereza anthu inu, koma musamvetsetse. Onani mobwerezabwereza, koma musazindikire chilichonse.’+

  • Yesaya 56:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Alonda ake ndi akhungu+ ndipo sakudziwa chilichonse.+ Onsewo ndi agalu opanda mawu. Satha kuuwa.+ Amangokhalira kupuma wefuwefu ndi kugona pansi. Amakonda kugona tulo.+

  • Yesaya 61:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 61 Mzimu wa Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, uli pa ine,+ pakuti Yehova wandidzoza+ kuti ndikanene uthenga wabwino kwa anthu ofatsa.+ Wandituma kuti ndikamange zilonda za anthu osweka mtima,+ ndikalengeze za ufulu kwa anthu ogwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina,+ ndiponso ndikatsegule maso a akaidi.+

  • Yeremiya 4:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Anthu anga ndi opusa.+ Iwo sanaganizire za ine.+ Iwo ndi ana opanda nzeru ndipo sazindikira kalikonse.+ Iwo ndi anzeru pa kuchita zoipa koma sadziwa kuchita zabwino.+

  • Ezekieli 12:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 “Iwe mwana wa munthu, ukukhala pakati pa anthu opanduka+ omwe ali ndi maso koma saona,+ omwe ali ndi makutu koma samva,+ chifukwa ndi anthu opanduka.+

  • Luka 4:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 “Mzimu wa Yehova+ uli pa ine, chifukwa iye anandidzoza kuti ndilengeze uthenga wabwino kwa osauka. Anandituma kudzalalikira za kumasulidwa kwa ogwidwa ukapolo, ndi zoti akhungu ayambe kuona. Anandituma kudzamasula oponderezedwa kuti akhale mfulu,+

  • 2 Akorinto 4:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Pakati pa anthu amenewa, mulungu wa nthawi* ino+ wachititsa khungu maganizo a anthu osakhulupirira,+ kuti asaone+ kuwala+ kwa uthenga wabwino waulemerero+ wonena za Khristu, yemwe ali chifaniziro+ cha Mulungu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena