43Tsopano iwe Yakobo, mvera zimene wanena Yehova Mlengi wako,+ yemwe anakupanga+ iwe Isiraeli. Iye wanena kuti: “Usachite mantha, pakuti ine ndakuwombola.+ Ndakuitana pokutchula dzina.+ Iwe ndiwe wanga.+
21 “Kumbukira zinthu zimenezi iwe Yakobo,+ ndiponso iwe Isiraeli, pakuti ndiwe mtumiki wanga.+ Ine ndiye amene ndinakuumba.+ Iweyo ndiwe mtumiki wanga. Iwe Isiraeli, ine sindikuiwala.+