22 Iwo anati: “Tachokera kwa Koneliyo, kapitawo wa asilikali. Iye ndi munthu wolungama ndi woopa Mulungu,+ amene mtundu wonse wa Ayuda umamuyamikira.+ Mngelo woyera anamupatsa malangizo a Mulungu kuti atume anthu kudzakutengani kuti mupite kunyumba kwake, akamve zimene inu mukanene.”