Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 3:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Pamenepo Mulungu anati: “Chifukwa ndidzakhala nawe.+ Ndipo chizindikiro chako chakuti ine ndi amene ndakutuma ndi ichi:+ Pambuyo powatulutsa anthuwo mu Iguputo, anthu inu mudzatumikira Mulungu woona paphiri lino.”+

  • Deuteronomo 31:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Limbani mtima ndipo chitani zinthu mwamphamvu.+ Musawaope kapena kuchita nawo mantha,+ chifukwa Yehova Mulungu wanu ndi amene akuyenda patsogolo panu. Iye sadzakutayani kapena kukusiyani ngakhale pang’ono.”+

  • Yoswa 1:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Palibe amene adzatha kulimbana nawe masiku onse a moyo wako.+ Ndidzakhala nawe+ monga mmene ndinakhalira ndi Mose, sindidzakutaya kapena kukusiya ngakhale pang’ono.+

  • Yeremiya 15:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 “Ndakuchititsa kukhala ngati mpanda wamkuwa wolimba kwambiri kwa anthu awa.+ Iwo adzamenyana nawe ndithu, koma sadzakugonjetsa,+ pakuti ine ndili ndi iwe kuti ndikupulumutse ndi kukulanditsa,”+ watero Yehova.

  • Machitidwe 18:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 chifukwa ine ndili nawe.+ Palibe munthu amene adzakukhudze ndi kukuvulaza, pakuti ndili ndi anthu ambiri mumzinda uno.”

  • Machitidwe 26:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Ndidzakuonetsa zimenezi pamene ndidzakulanditsa kwa anthu awa ndi kwa anthu a mitundu ina, kumene ine ndikukutumiza.+

  • 2 Akorinto 1:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Iye anatipulumutsadi ku chinthu choopsa, ndicho imfa, ndipo adzatipulumutsabe.+ Tikukhulupirira kuti iye apitiriza kutipulumutsa.+

  • Aheberi 13:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Moti tikhale olimba mtima ndithu+ ndipo tinene kuti: “Yehova* ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa. Munthu angandichite chiyani?”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena