-
Zefaniya 2:7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Chigawo chimenecho chidzakhala cha otsala a m’nyumba ya Yuda+ ndipo adzapezamo msipu. Madzulo iwo adzagona momasuka m’nyumba za mu Asikeloni. Zidzatero chifukwa chakuti Yehova Mulungu wawo adzawakumbukira+ ndipo adzasonkhanitsa ndi kubwezeretsa anthu awo omwe anagwidwa n’kutengedwa kupita ku ukapolo.”+
-
-
Zefaniya 3:20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Pa nthawi imeneyo ndidzakubwezaninso kunyumba anthu inu. Ndithu, pa nthawi imeneyo ndidzakusonkhanitsani pamodzi. Ndidzakuchititsani kukhala otchuka komanso otamandidwa pakati pa mitundu yosiyanasiyana padziko lapansi. Zimenezi zidzachitika ndikadzabwezeretsa pamaso pako anthu ako amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita ku ukapolo,” watero Yehova.+
-