Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 78:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  8 Ndipo asadzakhale ngati makolo awo,+

      M’badwo wosamva ndi wopanduka,+

      M’badwo umene sunakonze mtima wawo,+

      Ndipo maganizo awo sanali okhulupirika kwa Mulungu.+

  • Salimo 81:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Choncho ndinawasiya kuti apitirize kuumitsa mtima wawo.+

      Iwo anapitiriza kuyenda mu nzeru zawo.+

  • Yesaya 65:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 “Ndatambasula manja anga tsiku lonse kwa anthu amakani,*+ amene akuyenda m’njira yoipa+ potsatira maganizo awo,+

  • Yeremiya 3:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Pa nthawiyo mzinda wa Yerusalemu adzautcha kuti mpando wachifumu wa Yehova.+ Ndipo mitundu yonse adzaisonkhanitsira+ ku Yerusalemu kuti ikatamande dzina la Yehova+ kumeneko. Iwo sadzaumitsanso mitima yawo yoipayo.”+

  • Yeremiya 7:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Koma iwo sanamvere kapena kutchera khutu,+ ndipo anapitiriza kuyenda mwa zofuna zawo, mwa kuuma kwa mtima wawo woipawo,+ mwakuti anali kuyenda mobwerera m’mbuyo osati mopita patsogolo,+

  • Yeremiya 9:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 koma iwo anapitirizabe kuumitsa mitima yawo+ ndi kutsatira mafano a Baala,+ zinthu zimene anaphunzitsidwa ndi makolo awo.+

  • Zekariya 7:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Iwo anaumitsa mtima wawo+ ngati mwala wolimba kwambiri kuti asamvere malamulo+ ndi mawu a Yehova wa makamu, amene anawatumizira mwa mzimu wake+ kudzera mwa aneneri akale.+ Choncho Yehova wa makamu anakwiya kwambiri.”+

  • Aroma 10:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Koma za Aisiraeli iye anati: “Ndatambasula manja anga tsiku lonse kwa anthu osamva+ komanso otsutsa.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena