21 Kuwonjezera apo, asilikali amene wawalemba ganyu ali ngati ana a ng’ombe onenepa,+ koma iwonso agonja+ ndipo onse athawa. Sanathe kulimba+ pakuti tsiku lawo la tsoka ndiponso nthawi ya kulangidwa kwawo yafika.’+
44 Iwo adzakuwononga+ limodzi ndi ana ako amene ali mwa iwe. Ndipo sadzasiya mwala pamwala unzake+ mwa iwe, chifukwa sunazindikire kuti nthawi yokuyendera inali itakwana.”+