4 Usachite mantha,+ pakuti sudzachititsidwa manyazi.+ Usachite manyazi, pakuti sudzakhumudwitsidwa.+ Iwe udzaiwala ngakhale manyazi a paubwana wako,+ ndipo sudzakumbukiranso kunyozeka kwa paumasiye wako wa nthawi yaitali.”
14 “Ana a anthu okusautsa adzabwera kwa iwe atawerama.+ Onse amene anali kukuchitira chipongwe adzagwada pamapazi ako,+ ndipo adzakutcha mzinda wa Yehova, Ziyoni+ wa Woyera wa Isiraeli.