Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 23:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 “Zipatso zoyamba kucha zabwino koposa zam’munda mwanu muzibwera nazo kunyumba ya Yehova Mulungu wanu.+

      “Musawiritse mwana wa mbuzi mumkaka wa mayi wake.+

  • Numeri 3:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Pakuti mwana aliyense woyamba kubadwa ndi wanga.+ M’tsiku limene ndinapha mwana aliyense woyamba kubadwa m’dziko la Iguputo,+ ndinadzipatulira mwana aliyense woyamba kubadwa pakati pa Aisiraeli, kuyambira munthu mpaka chiweto.+ Amenewa azikhala anga. Ine ndine Yehova.”

  • Numeri 18:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 “Ndakupatsa iwe zipatso zoyambirira+ za mafuta onse abwino koposa, vinyo yense watsopano wabwino koposa, ndi mbewu zabwino koposa, zimene anthu azizipereka kwa Yehova.+

  • Numeri 18:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Chakhumicho ndicho chizikhala chopereka chanu, monga cha tirigu wochokera pamalo popunthira,+ ndi cha vinyo wochuluka wochokera mopondera mphesa, kapena cha mafuta ochuluka ochokera m’chofinyira mafuta.

  • Deuteronomo 18:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Uziperekanso gawo loyamba la mbewu zako, vinyo wako watsopano, mafuta ndi ubweya wa nkhosa wometedwa moyambirira.+

  • 2 Mbiri 31:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Kuwonjezera pamenepo, Hezekiya anauza anthu okhala mu Yerusalemu kuti apereke gawo loyenera kupita kwa ansembe+ ndi Alevi,+ n’cholinga choti iwo azitsatira+ mosamala chilamulo cha Yehova.+

  • 2 Mbiri 31:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Ndiyeno Azariya,+ wansembe wamkulu wa nyumba ya Zadoki,+ anamuyankha kuti: “Kuyambira pamene anthu anayamba kubweretsa zopereka+ m’nyumba ya Yehova, pakhala kudya ndi kukhuta+ ndipo pali zotsala zambiri,+ chifukwa Yehova wadalitsa anthu ake+ ndipo zonse mukuzionazi n’zimene zatsala.”

  • Nehemiya 10:35
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 35 Tinachita maerewo kuti tipezenso wobweretsa kunyumba ya Yehova zipatso zoyamba kucha m’dziko lathu+ chaka ndi chaka, ndi zipatso zoyamba kucha mwa zipatso zonse za mtengo uliwonse.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena