20 Ndiyeno munthu uja anandiuza kuti: “Amenewa ndi malo amene ansembe aziwiritsirapo nsembe ya kupalamula+ ndi nsembe yamachimo,+ komanso pamene aziphikirapo nsembe yambewu.+ Aziphikira pamenepa kuti asamatulutse chilichonse kupita nacho kubwalo lakunja ndi kuyeretsa anthu.”+