15 Chotero iye anatengera Yehoyakini+ ku Babulo.+ Anatenga ku Yerusalemu mayi a mfumuyo,+ akazi ake, nduna za panyumba yake,+ ndi akuluakulu a m’dzikolo, n’kuwapititsa ku Babulo.
11 “Pakuti ine ndili ndi iwe kuti ndikupulumutse,”+ watero Yehova. “Ndidzawononga anthu a mitundu yonse ya kumene ndinakubalalitsirani,+ koma iwe sindidzakuwononga.+ Ndidzakuwongolera pa mlingo woyenera chifukwa sindidzakusiya osakulanga.”+