17 Iyo idzafika motsimikiza mtima+ kwambiri pamodzi ndi gulu lankhondo lamphamvu la ufumu wake. Adzachita nayo mgwirizano+ ndipo idzakwaniritsa zolinga zake.+ Iyo idzaloledwa kuti iwononge mwana wamkaziyo. Mwana wamkaziyo sadzapirira ndipo sadzapitiriza kukhala wokhulupirika kwa iyo.+